|
| 1 |
|
| “Itana ngati ungathe, koma ndani adzakuyankhe? Kodi ndi kwa mngelo uti ungapezeko thandizo? |
|
| 2 |
|
| Mkwiyo umapha chitsiru, ndipo njiru imawononga wopusa. |
|
| 3 |
|
| Ine ndinaona chitsiru chitamera mizu, koma mwadzidzidzi nyumba yake inatembereredwa. |
|
| 4 |
|
| Ana ake alibe ndi chitetezo chomwe; amaponderezedwa mʼbwalo la milandu popanda owateteza. |
|
| 5 |
|
| Anthu anjala amamudyera zokolola zake, amamutengera ndi za pa minga pomwe, ndipo anthu akhwinthi amafunkha chuma chake. |
|
| 6 |
|
| Pakuti masautso satuluka mʼfumbi, ndipo kuwukira sikuchokera mʼdothi. |
|
| 7 |
|
| Komatu munthu amabadwira kuti azunzike monga momwe mbaliwali zimathethekera mlengalenga. |
|
| 8 |
|
| “Koma ndikanakhala ine, ndikanamudandawulira Mulungu; ndikanapereka mlandu wanga kwa Iye. |
|
| 9 |
|
| Iye amachita zozizwitsa zimene sizimvetsetseka, zodabwitsa zimene sizingatheke kuwerengedwa. |
|
| 10 |
|
| Iye amagwetsa mvula pa dziko lapansi, ndipo amathirira minda ya anthu. |
|
| 11 |
|
| Iye amakweza anthu wamba, ndipo iwo amene akulira amawayika pa malo otetezedwa. |
|
| 12 |
|
| Iyeyo amalepheretsa chiwembu cha anthu ochenjera, kotero kuti cholinga chawo sichipindula kanthu. |
|
| 13 |
|
| Iye amakola anthu ochenjera mu msampha wa kuchenjera kwawo, ndipo zolinga za atambwali amazithetsa msangamsanga. |
|
| 14 |
|
| Mdima umawagwera nthawi yamasana; nthawi yamasana amayenda moyambasayambasa monga nthawi ya usiku. |
|
| 15 |
|
| Mulungu amapulumutsa amphawi ku lupanga la mʼkamwa mwawo; amawapulumutsa mʼmanja mwa anthu amphamvu. |
|
| 16 |
|
| Choncho osauka ali ndi chiyembekezo, ndipo anthu opanda chilungamo amawatseka pakamwa. |
|
| 17 |
|
| “Wodala munthu amene Mulungu amamudzudzula; nʼchifukwa chake usanyoze chilango cha Wamphamvuzonse. |
|
| 18 |
|
| Pakuti Iye amavulaza koma amamanganso mabalawo; Iye amakantha munthu, komanso manja ake amachiritsa. |
|
| 19 |
|
| Pakuti adzakupulumutsa ku masautso nthawi ndi nthawi, mavuto angachuluke bwanji, sadzakukhudza ndi pangʼono pomwe. |
|
| 20 |
|
| Pa nthawi ya njala adzakulanditsa ku imfa, ndipo nthawi ya nkhondo adzakupulumutsa ku lupanga. |
|
| 21 |
|
| Adzakuteteza kwa anthu osinjirira, ndipo palibe chifukwa chochitira mantha pamene chiwonongeko chafika. |
|
| 22 |
|
| Uzidzaseka pa nthawi ya chiwonongeko ndi ya njala, ndipo palibe chifukwa chochitira mantha ndi zirombo za mʼdziko lapansi. |
|
| 23 |
|
| Pakuti udzachita pangano ndi miyala ya mʼmunda mwako, ndipo nyama zakuthengo zidzakhala nawe mwamtendere. |
|
| 24 |
|
| Udzadziwa kuti nyumba yako ndi malo otetezedwa; udzawerengera katundu wako ndipo sudzapeza kanthu kamene kasowapo. |
|
| 25 |
|
| Udzadziwa kuti ana ako adzakhala ambiri, ndipo zidzukulu zako zidzakhala ngati udzu wa mʼdziko lapansi. |
|
| 26 |
|
| Udzafika ku manda utakalamba, monga mitolo ya zokolola pa nyengo yake. |
|
| 27 |
|
| “Ife tafufuza zimenezi ndipo ndi zoona, choncho uzimvere ndi kuzitsata.” |
|
|
|
|