|
| 1 |
|
| Tsono Yobu anayankha kuti, |
|
| 2 |
|
| “Achikhala mavuto anga anayezedwa, ndipo zipsinjo zanga zonse zikanayikidwa pa sikelo! |
|
| 3 |
|
| Ndithu, zikanalemera kupambana mchenga wa ku nyanja; nʼchifukwa chake mawu anga akhala okhadzula. |
|
| 4 |
|
| Mivi ya Wamphamvuzonse yandibaya, thupi langa likumva ululu wa miviyo; zoopsa za Mulungu zandizinga. |
|
| 5 |
|
| Kodi bulu wakuthengo amalira akakhala ndi msipu, nanga ngʼombe imalira ikakhala ndi chakudya? |
|
| 6 |
|
| Kodi chakudya chosakoma nʼkuchidya chopanda mchere, nanga choyera cha dzira chimakoma? |
|
| 7 |
|
| Zakudya zimenezi sindifuna nʼkuzilawa komwe; zakudya zimenezi zimabwerera kukhosi. |
|
| 8 |
|
| “Aa, ndikanalandira chimene ndikuchipempha, chikhala Mulungu anandipatsa chimene ndikuchiyembekezera, |
|
| 9 |
|
| achikhala chinamukomera Mulungu kuti anditswanye, kulola dzanja lake kuti lindimenye ndi kundiwonongeratu! |
|
| 10 |
|
| Pamenepo ine ndikanakhalabe ndi chitonthozo ichi, ndikanakondwa mu ululu wanga wosalekezawu podziwa kuti sindinakane mawu a Woyerayo. |
|
| 11 |
|
| “Kodi mphamvu zanga nʼzotani kuti ndizikhalabe ndi chiyembekezo? Nanga zoyembekezera zanga nʼzotani kuti ndipirirebe? |
|
| 12 |
|
| Kodi ine ndili ndi mphamvu? Nanga thupi langa ndi lolimba ngati chitsulo? |
|
| 13 |
|
| Kodi ndili ndi mphamvu zodzithandizira ndekha, nanga pakuti thandizo lachotsedwa kwa ine? |
|
| 14 |
|
| “Munthu amene ali kakasi ayenera kukhala ndi abwenzi odzipereka, ngakhale kuti iyeyo wasiya kuopa Wamphamvuzonse. |
|
| 15 |
|
| Koma abale anga ndi wosadalirika ngati mitsinje yowuma msanga, ngati mitsinje imene imathamanga. |
|
| 16 |
|
| Ali ngati mitsinje ya madzi akuda nthawi ya dzinja, imene madzi ake amakhala ambiri chifukwa chakuchuluka kwa mvula, |
|
| 17 |
|
| koma madziwo amasiya kuyenda nthawi yachilimwe, ndipo nthawi yotentha madziwo amawumiratu mʼmitsinjemo. |
|
| 18 |
|
| Anthu oyenda pa ngamira amapatukirako kufuna madzi; iwo amangoyendayenda nʼkufera mʼchipululu. |
|
| 19 |
|
| Anthu oyenda pa ngamira a ku Tema amafunafuna madzi, anthu amalonda apaulendo a ku Seba amafunafuna mwa chiyembekezo. |
|
| 20 |
|
| Amataya mtima chifukwa ankayembekezera kupeza madzi; koma akafika kumeneko, amangokhumudwako. |
|
| 21 |
|
| Tsono inunso mukuonetsa kuti ndinu osathandiza, mukuona chinthu choopsa kwambiri ndipo mukuchita mantha. |
|
| 22 |
|
| Kodi ine ndinanenapo kuti, ‘Ndiperekereni kenakake, ndilipirireni dipo kuchokera pa chuma chanu, |
|
| 23 |
|
| ndilanditseni mʼdzanja la mdani, ndiwomboleni mʼdzanja la munthu wankhanza?’ |
|
| 24 |
|
| “Phunzitseni, ndipo ine ndidzakhala chete; ndionetseni pomwe ndalakwitsa. |
|
| 25 |
|
| Ndithu, mawu owona ndi opweteka! Koma mawu anu otsutsa akufuna kuonetsa chiyani? |
|
| 26 |
|
| Kodi inu mukufuna kundidzudzula pa zimene ndikunena, ndipo mukufuna kuyesa mawu a munthu wosweka mtima ngati mphepo chabe? |
|
| 27 |
|
| Inu mungathe kuchita maere kuti mugulitse ana amasiye ndi kumugulitsa bwenzi lanu. |
|
| 28 |
|
| “Koma tsopano ndichitireni chifundo pamene mukundiyangʼana. Kodi ine ndingayankhule zabodza pamaso panu? |
|
| 29 |
|
| Fewani mtima, musachite zosalungama; ganiziraninso popeza chilungamo changa chikanalipobe. |
|
| 30 |
|
| Kodi pali choyipa chilichonse pa milomo yanga? Kodi pakamwa panga sipangathe kuzindikira kanthu koyipa? |
|
|
|
|