|
| 1 |
|
| Tsono Yobe adayankha kuti, |
|
| 2 |
|
| “Achikhala mavuto anga adaayesedwa, achikhala masoka anga adaaŵaika pa sikelo, |
|
| 3 |
|
| bwenzi atalemera kupambana mchenga wonse wam'nyanja. Nchifukwa chake kulankhula kwanga kuli kokadzulira. |
|
| 4 |
|
| Zoonadi mivi yake ya Mphambe yandibaya, thupi langa likumva ululu wa miviyo. Zoopsa za Mulungu zandizinga, kuti zilimbane nane. |
|
| 5 |
|
| Kodi bulu amalira akakhala ndi msipu? Nanga ng'ombe, kodi imalira ikakhala ndi chakudya? |
|
| 6 |
|
| Kodi chakudya nkuchidya chili zii, chopanda mchere? Kodi choyera cha dzira chimatsekemera? |
|
| 7 |
|
| Zakudya zimenezi sindifuna nkuzilaŵa komwe, zakudya zake ndi zobwerera kukhosi. |
|
| 8 |
|
| “Achikhala ndidaalandira chomwe ndikufuna, achikhala Mulungu adaandipatsa chimene ndikukhumba! |
|
| 9 |
|
| Achikhala kudaamkomera Mulungu kuti anditswanye, achikhala adaandimenya ndi dzanja lake, nkundiwonongeratu! |
|
| 10 |
|
| Zimenezi zikadandisangalatsa, ndikadakondwa nazo kwambiri ngakhale zipweteke chotani, podziŵa kuti sindidakane mau a Woyera uja. |
|
| 11 |
|
| Kodi mphamvu zanga ndi zotani kuti ndizikhalabe ndi moyo? Nanga moyo wanga ukupitiriranji, ngati chiyembekezo palibe? |
|
| 12 |
|
| Kodi ine ndidachita kuti gwa ngati mwala? Kodi thupi langa ndi lolimba ngati chitsulo? |
|
| 13 |
|
| Zoona, ndilibenso mphamvu zodzipulumutsira, kulibenso kwina koti nkupezerako chithandizo. |
|
| 14 |
|
| “Pa mavuto ngati ameneŵa pafunika abwenzi okhulupirika, kuwopa kuti mwina mwake munthu angasiyane ndi Mphambe. |
|
| 15 |
|
| Koma abwenzi anga ndi onyenga, ngati mtsinje wothamanga, ngati mitsinje youma msanga mvula ikasoŵa. |
|
| 16 |
|
| Ali ngati mitsinje ya madzi abii nthaŵi ya dzinja, imene madzi ake amakhala ambiri chifukwa cha kuchuluka kwa mvula. |
|
| 17 |
|
| Koma pa nthaŵi ya mafundi imauma, kukatentha imamwerera. |
|
| 18 |
|
| Anthu apaulendo amapatukirako kufuna madzi, koma amangoyendayenda nkufera m'chipululu. |
|
| 19 |
|
| Oyenda pa ngamira a ku Tema amaifunafuna mitsinjeyo. Alendo a ku Sheba amaidalira. |
|
| 20 |
|
| Amataya mtima chifukwa ankayembekeza kupeza madzi, koma pofika kumeneko, angoti kakasi, poti idauma. |
|
| 21 |
|
| “Tsono umu ndimo m'mene inuyo mwandichitira ine. Mwaona tsoka langa, ndipo mukuchita mantha. |
|
| 22 |
|
| Kodi ndanena kuti, ‘Mundipatse mphatso,’ kapena kuti, ‘Mupereke chiphuphu kwa wina chifukwa cha ine?’ |
|
| 23 |
|
| Kodi ndanena kuti, ‘Mundipulumutse kwa mdani,’ kapena kuti, ‘Mundiwombole kwa ondizunza?’ |
|
| 24 |
|
| “Chabwino, langizeni ndipo ndidzakhala chete. Dziŵitseni m'mene ndidachimwira. |
|
| 25 |
|
| Mau oona amalasa mtima, koma inu mukunditsutsa pa zotani? |
|
| 26 |
|
| Kodi inu mukufuna kundidzudzuliranji? Monga simukuwona kuti mau a munthu wotaya mtima ndi mphepo chabe? |
|
| 27 |
|
| Zoonadi inu mumapondereza ana amasiye, ndi kuŵaika pa malonda abwenzi anu omwe. |
|
| 28 |
|
| “Tsono mundiyang'anitsitse bwino! Sindikulankhula zabodza pamaso panu. |
|
| 29 |
|
| Chonde, feŵani mtima, musachite zosalungama. Musandiimbe mlandu, poti ndine wolungama. |
|
| 30 |
|
| Kodi mukuganiza kuti ndikulankhula zabodza? Monga ine sindingasiyanitse chabwino ndi choipa?” |
|
|
|
|