|
| 1 |
|
| Pamenepo Bilidadi wa ku Suki anayankha kuti, |
|
| 2 |
|
| “Kodi udzakhala ukuyankhula zoterezi mpaka liti? Mawu ako ali ngati mphepo yamkuntho. |
|
| 3 |
|
| Kodi Mulungu amapotoza chiweruzo cholungama? Kodi Wamphamvuzonse amalephera kuchita zachilungamo? |
|
| 4 |
|
| Pamene ana ako anamuchimwira Mulungu, Iye anawapereka kuti alangidwe chifukwa cha tchimo lawo. |
|
| 5 |
|
| Koma utayangʼana kwa Mulungu, ndi kudandaulira Wamphamvuzonse, |
|
| 6 |
|
| ngati uli wangwiro ndi wolungama mtima ngakhale tsopano Iye adzachitapo kanthu mʼmalo mwako ndipo adzakubwezeretsa pa malo ako oyenera. |
|
| 7 |
|
| Chiyambi chako chidzaoneka ngati chochepa koma chimaliziro chako chidzakhala chopambana. |
|
| 8 |
|
| “Funsa kwa anthu amvulazakale ndipo upeze zimene makolo awo anaziphunzira |
|
| 9 |
|
| pakuti ife ndife ana adzulodzuloli ndipo sitidziwa chilichonse, ndipo moyo wathu pa dziko lapansi uli ngati chithunzithunzi. |
|
| 10 |
|
| Kodi iwo sadzakulangiza ndi kukufotokozera? Kodi sadzakuwuza mawu ochokera pa zimene amazidziwa? |
|
| 11 |
|
| Kodi bango nʼkumera pa nthaka yopanda chinyontho? Nanga mawango nʼkukula bwino popanda madzi? |
|
| 12 |
|
| Popanda madzi, zimenezi zimafota zikanali zaziwisi ndi zosadula; zimawuma msangamsanga kuposa bango. |
|
| 13 |
|
| Ndimo mmene amachitira anthu onse amene amayiwala Mulungu; ndi mmene chiyembekezo cha munthu wosapembedza Mulungu chimathera. |
|
| 14 |
|
| Kulimba mtima kwake kumafowoka; zimene iye amadalira zili ngati ukonde wa kangawude. |
|
| 15 |
|
| Iye amatsamira ukonde wake, koma umaduka; amawugwiritsitsa koma sulimba. |
|
| 16 |
|
| Munthu woyipayo ali ngati chomera chothiriridwa bwino chimene chili pa dzuwa, nthambi zake zimatambalala pa munda wake; |
|
| 17 |
|
| mizu yake imayanga pa mulu wa miyala ndi kufunafuna malo woti izikike pa miyalapo. |
|
| 18 |
|
| Koma pamene yachotsedwa pamalo pakepo, pamalopo pamakana chomeracho ndi kuti, ‘Ine sindinakuonepo.’ |
|
| 19 |
|
| Ndithudi chomeracho chimafota, ndipo pa nthakapo pamatuluka zomera zina. |
|
| 20 |
|
| “Ndithudi, Mulungu sakana munthu amene alibe cholakwa kapena kulimbikitsa anthu ochita zoyipa. |
|
| 21 |
|
| Iye adzadzaza mʼkamwa mwako ndi phwete ndipo milomo yako idzafuwula ndi chimwemwe. |
|
| 22 |
|
| Adani ako adzachita manyazi, ndipo malo okhalamo anthu oyipa sadzaonekanso.” |
|
|
|
|