|
| 1 |
|
| Ndipo Yobu anayankha kuti, |
|
| 2 |
|
| “Zoonadi, ndikudziwa kuti zimenezi ndi zoona. Koma munthu angathe bwanji kukhala wolungama pamaso pa Mulungu? |
|
| 3 |
|
| Ngakhale wina atafuna kutsutsana naye, Iye sangamuyankhe munthuyo ngakhale mawu amodzi omwe. |
|
| 4 |
|
| Mulungu ndi wa nzeru zambiri ndipo mphamvu zake ndi zochuluka. Ndani analimbana naye popanda kupwetekeka? |
|
| 5 |
|
| Iye amasuntha mapiri, mapiriwo osadziwa, ndipo amawagubuduza ali wokwiya. |
|
| 6 |
|
| Iye amagwedeza dziko lapansi kulisuntha pamalo pake ndipo amanjenjemeretsa mizati yake. |
|
| 7 |
|
| Iye amayankhula ndi dzuwa ndipo siliwala; Iyeyo amaphimba kuwala kwa nyenyezi. |
|
| 8 |
|
| Ndi Mulungu yekha amene anayala mayiko akumwamba ndipo amayenda pa mafunde a pa nyanja. |
|
| 9 |
|
| Iye ndiye mlengi wa nyenyezi zamlalangʼamba ndi akamwiniatsatana, nsangwe ndi kumpotosimpita. |
|
| 10 |
|
| Iye amachita zozizwitsa zimene sizimvetsetseka, zodabwitsa zimene sizingawerengeke. |
|
| 11 |
|
| Akapita pafupi ndi ine sindingathe kumuona; akadutsa, sindingathe kumuzindikira. |
|
| 12 |
|
| Ngati Iye alanda zinthu, ndani angathe kumuletsa? Ndani anganene kwa Iye kuti, ‘Mukuchita chiyani?’ |
|
| 13 |
|
| Mulungu sabweza mkwiyo wake; ngakhale gulu lankhondo la Rahabe linawerama pa mapazi ake. |
|
| 14 |
|
| “Nanga ine ndingathe kukangana naye bwanji? Ndingawapeze kuti mawu oti nʼkutsutsana naye? |
|
| 15 |
|
| Ngakhale nditakhala wosalakwa, sindingamuyankhe; ndikanangopempha chifundo kwa woweruza wanga. |
|
| 16 |
|
| Ngakhale ndikanamuyitana ndipo Iye ndi kuvomera, sindikhulupirira kuti akanamva mawu angawo. |
|
| 17 |
|
| Iye akanandikantha ndi mphepo yamkuntho, ndipo akanandipweteka popanda chifukwa. |
|
| 18 |
|
| Mulungu sakanandilola kuti ndipumenso koma akanandichulukitsira zowawa. |
|
| 19 |
|
| Tikanena za mphamvu, Iye ndi wamphamvudi! Ndipo tikanena za chiweruzo cholungama, ndani angamuzenge mlandu? |
|
| 20 |
|
| Ngakhale ndikanakhala wosalakwa, zoyankhula zanga zikananditsutsa; ndikanakhala wopanda cholakwa, pakamwa panga pakanandipeza wolakwa. |
|
| 21 |
|
| “Ngakhale ine ndili wosalakwa, sindidziyenereza ndekha; moyo wanga ndimawupeputsa. |
|
| 22 |
|
| Zonse nʼzofanana; nʼchifukwa chake ndikuti, ‘Iye amawononga anthu osalakwa ndi anthu oyipa omwe.’ |
|
| 23 |
|
| Pamene mkwapulo ubweretsa imfa yadzidzidzi, Iye amaseka tsoka la munthu wosalakwayo. |
|
| 24 |
|
| Pamene dziko lagwa mʼmanja mwa anthu oyipa Iye amawatseka maso anthu oweruza dzikolo. Ngati si Iyeyo, nanga ndani? |
|
| 25 |
|
| “Masiku anga ndi othamanga kwambiri kupambana munthu waliwiro; masikuwo amapita ine osaonapo zabwino. |
|
| 26 |
|
| Amayenda ngati mabwato a njedza pa nyanja, ngati mphungu zothamangira nyama zoti zidye. |
|
| 27 |
|
| Nʼtanena kuti, ‘Ndidzayiwala madandawulo anga, ndidzasintha nkhope yanga ndipo ndidzasekerera,’ |
|
| 28 |
|
| ndikuopabe mavuto anga onse, popeza ndikudziwa kuti simudzavomereza kuti ndine wosalakwa. |
|
| 29 |
|
| Popeza ndapezeka kale wolakwa ndivutikirenji popanda phindu? |
|
| 30 |
|
| Ngakhale nditasamba mʼmadzi oyera kwambiri ndi kusamba mʼmanja mwanga ndi sopo, |
|
| 31 |
|
| mutha kundiponyabe pa dzala, kotero kuti ngakhale zovala zanga zomwe zidzandinyansa. |
|
| 32 |
|
| “Mulungu si munthu ngati ine kuti ndithe kumuyankha, sindingathe kutsutsana naye mʼbwalo la milandu. |
|
| 33 |
|
| Pakanapezeka munthu wina kuti akhale mʼkhalapakati wathu, kuti atibweretse ife tonse pamodzi, |
|
| 34 |
|
| munthu wina woti achotse ndodo ya Mulungu pa ine kuti kuopsa kwake kusandichititsenso mantha! |
|
| 35 |
|
| Pamenepo ine ndikanatha kuyankhula mosamuopa Mulunguyo, koma monga zililimu, sindingathe. |
|
|
|
|