|
| 1 |
|
| Tsono Yobe adayankha kuti, |
|
| 2 |
|
| “Inde, ndikudziŵa kuti zimenezi ndi zoona, koma nanga munthu angathe bwanji kukhala wolungama pamaso pa Mulungu? |
|
| 3 |
|
| Kodi wina aliyense angathe kutsutsana ndi Mulungu? Ai sangathe kutsutsana naye, chifukwa Mulungu ali ndi mafunso ambiri osayankhika. |
|
| 4 |
|
| Mulungu ndi wanzeru, ndipo ndi wamphamvu kwambiri. Palibe munthu amene angathe kulimbana naye, popanda kupwetekerapo. |
|
| 5 |
|
| Iyeyo amasendeza mapiri, iwo osadziŵako, amaŵagubuduza ali wokwiya. |
|
| 6 |
|
| Ndiye amene amagwedeza dziko lapansi ndi zivomezi, ndipo mizati yake imanjenjemera. |
|
| 7 |
|
| Ndiye amene angalamule dzuŵa kuti lisatuluke m'maŵa, ndi kuletsa nyenyezi kuti zisaŵale usiku. |
|
| 8 |
|
| Ndi Mulungu yekha amene adayala zakuthambo, ndiye amayenda pa mafunde apanyanja. |
|
| 9 |
|
| Ndiye amene adalenga nyenyezi za Mlalang'amba ndi Akamwiniatsatana, Nsangwe ndi Kumpotosimpita. |
|
| 10 |
|
| Ndiye amene amachita zazikulu zosamvetseka, ndiye amene amachita zodabwitsa zosaŵerengeka. |
|
| 11 |
|
| Ndithu Mulungu akapita pafupi ndi ine, sindimuwona konse. Akandidutsa, ine sindimpenya. |
|
| 12 |
|
| Akamalanda zinthu, ndani angathe kumletsa? Ndani angathe kumufunsa kuti, ‘Mukuchita chiyani?’ |
|
| 13 |
|
| “Mulungu sabweza ukali wake, adaononga adani ake othandizana ndi Rahabu, chilombo choipa chija. |
|
| 14 |
|
| Nanga ineyo ndingathe kumuyankha bwanji? Mau okangana naye ndingaŵapeze kuti? |
|
| 15 |
|
| Ngakhale ndine wosachimwa, sindingathe kumuyankha Mulungu. Ndiyenera kungopempha chifundo kwa Iye amene akundizenga mlandu. |
|
| 16 |
|
| Ngakhale ndikadamuitana, Iye nkuvomera, sindikhulupirira kuti akadamvadi mau angawo. |
|
| 17 |
|
| Paja amandikantha ndi mavuto onga mphepo yamkuntho, amandipweteka ndi mabala ambiri, popanda nchifukwa chomwe. |
|
| 18 |
|
| Mulungu sandilola kuti ndipume, koma amandichulukitsirachulukitsira zoŵaŵa. |
|
| 19 |
|
| Kodi ine nkulimbana ndi Mulungu, mphamvu zonse zija? Kodi ine nkutsutsana ndi Mulungu pa bwalo la milandu? Ndani angamuzenge mlandu? |
|
| 20 |
|
| Ngakhale ndine wosalakwa, komabe zolankhula zanga zikhoza kunditsutsa. Ngakhale ndine wopanda cholakwa, akadandipezabe kuti ndine wolakwa. |
|
| 21 |
|
| Ine ndiye ndilibe mlandu, koma sindidziyenereza, moyo wanga ndimaunyoza. |
|
| 22 |
|
| Palibe chabwino ai. Nchifukwa chake ndikuti, Mulungu amaononga anthu oipa ndi anthu abwino omwe. |
|
| 23 |
|
| Pamene munthu wosachimwa afa mwadzidzidzi, Mulungu amangoseka tsoka la munthu wosachimwayo. |
|
| 24 |
|
| Mulungu akapereka dziko m'manja mwa anthu oipa, amaŵatseka maso anthu oweruza dzikolo. Ngati si Iyeyo wachita zimenezi, nanga nkukhala yani? |
|
| 25 |
|
| “Masiku anga ndi othamanga kwambiri kupambana munthu waliŵiro. Masikuwo amapita, ine osaona zabwino. |
|
| 26 |
|
| Amayenda ngati zombo zaliŵiro zapanyanja, ngati mphungu yogudukira nyama yoti idye. |
|
| 27 |
|
| Mwina ndinganene kuti, ‘Ndidzaiŵala madandaulo anga, nkhope yanga sidzakhalanso yachisoni, ndipo ndidzasangalala.’ |
|
| 28 |
|
| Koma ndimaopabe kuti mavuto anga onse adzabwereranso pa ine, pakuti ndikudziŵa kuti Mulungu sadzavomereza kuti ine ndine wosalakwa. |
|
| 29 |
|
| Ngati ndine wolakwa ndithu, chabwinotu, zagwa zatha! |
|
| 30 |
|
| Ngakhale ndisambe thupi lonse ndi madzi oyera kwambiri, ndi kusamba m'manja ndi sopo, |
|
| 31 |
|
| Mulungu adzandiponyabe pa dzala, ndipo zovala zanga zomwe zidzachita nane nyansi. |
|
| 32 |
|
| Zoona, Mulungu si munthu ngati ine, kuti ndingakangane naye, sindingathe kutsutsana naye pa mlandu. |
|
| 33 |
|
| Palibe mkhalapakati woti nkutiweruza aŵirife, woti nkugamula mlandu pakati pa Mulungu ndi ine. |
|
| 34 |
|
| Mulungu asandilange ndi ndodo yake, kuwopa Iye kusandidetse nkhaŵa. |
|
| 35 |
|
| Motero ndidakatha kulankhula osamuwopa, koma monga zilirimu, sindingathe konse.” |
|
|
|
|