Buku Lopatulika 1992
|
| 1 |
| Muimiranji patari, Yehova? Mubisaliranji m'nyengo za nsautso? |
| 2 |
| Podzikuza woipa apsereza waumphawi; Agwe m'ciwembu anapanganaco. |
| 3 |
| Pakuti woipa adzitamira cifuniro ca moyo wace, Adalitsa wosirira, koma anyoza Yehova. |
| 4 |
| Woipa, monga mwa kudzikuza kwa nkhope yace, akuti, Sadzafunsira. Malingaliro ace onse akuti, Palibe Mulungu. |
| 5 |
| Mayendedwe ace alimbika nthawi zonse; Maweruzo anu ali pamwamba posaona iye; Adani ace onse awanyodola. |
| 6 |
| Ati mumtima mwace, Sindidzagwedezeka ine; Ku mibadwo mibadwo osagwa m'tsoka ine. |
| 7 |
| M'kamwa mwace mwadzala kutemberera ndi manyengo ndi kucenjerera; Pansi pa lilime lace pali cibvutitso copanda pace. |
| 8 |
| Akhala m'molalira midzi; Mobisalamo akupha munthu wosacimwa: Ambisira waumphawi nkhope yace, |
| 9 |
| Alalira monga mkango m'ngaka mwace; Alalira kugwira wozunzika: Agwira wozunzika, pakumkola m'ukonde mwace. |
| 10 |
| Aunthama, nawerama, Ndipo aumphawi agwa m'zala zace. |
| 11 |
| Anena m'mtima mwace, Mulungu waiwala; Wabisa nkhope yace; sapenya nthawi zonse, |
| 12 |
| Ukani, Yehova; samulani dzanja lanu, Mulungu; Musaiwale ozunzika. |
| 13 |
| Woipa anyozeranii Mulungu, Anena m'mtima mwace, Simudzafunsira? |
| 14 |
| Mwapenya; pakuti mumayang'anira cibvutitso ndi cisoni kuti acipereke m'manja mwanu; Waumphawi adzipereka kwa Inu; Wamasiye mumakhala mthandizi wace. |
| 15 |
| Thyolani mkono wa woipa; Ndipo wocimwa, mutsate coipa cace kufikira simucipezanso cina. |
| 16 |
| Yehova ndiye Mfumu ku nthawi yamuyaya; Aonongeka amitundu m'dziko lace. |
| 17 |
| Yehova, mwamva cikhumbo ca ozunzika: Mudzakhazikitsa mtima wao, mudzachereza khutu lanu: |
| 18 |
| Kuti muweruze mlandu wa amasiye ndi wokhalira mphanthi, Kuti munthu wa pa dziko lapansi angaonjeze kuopsa. |
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa1992/psalms/010.mp3
150
10