×

Buku Loyera

MASALIMO 10

1
Chifukwa chiyani mumaima kutali nafe, Inu Chauta? Chifukwa chiyani mumabisala pamene tili pa mavuto?
2
Anthu oipa amazunza anthu osauka modzikuza. Akodwe m'misampha yotcha iwo omwe.
3
Paja munthu woipa amanyadira zokhumba za mtima wake, wokonda chuma amanyoza ndi kukana Chauta.
4
Munthu woipa sasamala Mulungu chifukwa cha kunyada kwake. Mumtima mwake amati, “Kulibe Mulungu.”
5
Zinthu zimamuyendera bwino nthaŵi zonse. Chiweruzo chanu chili naye kutali, ndipo salabadako konse. Kunena za adani ake, iye amangoŵanyodola.
6
Mumtima mwake amaganiza kuti, “Sindidzagwedezeka, sindidzaona konse mavuto.”
7
Pakamwa pake pamangolankhula zotemberera, zonyenga ndi zoopseza. M'kamwa mwake mumatuluka zovutitsa ena ndiponso zoipa zokhazokha.
8
Amalalira m'midzi, amapha anthu osalakwa m'malo obisalira. Amazondazonda kuti apeze opanda mwai.
9
Amabisalira osauka ngati mkango m'ngaka yake, amabisalira osauka kuti aŵagwire. Osaukawo amaŵagwiradi akaŵakokera mu ukonde wake.
10
Amambwandira ndi kupsitiriza anthu osoŵa mwai, ndipo nyonga zake zimaŵagwetsa pansi.
11
Mumtima mwake amaganiza kuti, “Mulungu sasamalako, waphimba maso ake, sadzaziwona zimenezi.”
12
Dzambatukani, Inu Chauta. Onetsani mphamvu zanu, Inu Mulungu. Musaiŵale ozunzika.
13
Chifukwa chiyani munthu woipa amanyoza Mulungu? Chifukwa chiyani mumtima mwake amati, “Sadzandilanga?”
14
Inutu mumaonadi, mumazindikira zovuta ndi zosautsa, kuti muchitepo kanthu. Wopanda mwai amadzipereka kwa Inu. Nayenso wamasiye mumamthandiza.
15
Thetsani mphamvu za munthu woipa ndi wochimwa. Fufuzani kuipa kwake, ndipo mumlange kuti asadzabwerezenso.
16
Chauta ndiye Mfumu mpaka muyaya. Mitundu ya anthu akunja idzatheratu m'dziko lake.
17
Chauta, mumamva zimene odzichepetsa amapempha. Mudzalimbitsa mitima yao, mudzaŵatchera khutu.
18
Potero mudzaŵateteza amasiye ndi opsinjidwa, kuti anthu amene ali a pansi pano, asadzathe kuwopsezanso.
Chewa Bible BLYDC
Bible Society of Malawi
:
Sungani Zolemba