Mawu a Mulungu 2016
|
| 1 |
| Salimo. Nyimbo yothokoza. Fuwulani kwa Yehova mwachimwemwe, inu dziko lonse lapansi. |
| 2 |
| Mulambireni Yehova mosangalala; bwerani pamaso pake ndi nyimbo zachikondwerero. |
| 3 |
| Dziwani kuti Yehova ndi Mulungu. Iye ndiye amene anatipanga ndipo ife ndife ake; ndife anthu ake, nkhosa za pabusa pake. |
| 4 |
| Lowani ku zipata zake ndi chiyamiko ndi ku mabwalo ake ndi matamando; muyamikeni ndi kutamanda dzina lake. |
| 5 |
| Pakuti Yehova ndi wabwino ndipo chikondi chake ndi chamuyaya; kukhulupirika kwake nʼkokhazikika pa mibado ndi mibado. |
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2016/psalms/100.mp3
150
100