×

Buku Lopatulika 1992

MASALIMO 101

1
Ndidzayimba za cifundo ndi ciweruzo; Ndidzayimba zakukulemekezani Inu, Yehova.
2
Ndidzacita mwanzeru m'njira yangwiro; Mudzandidzera liti? Ndidzayenda m'nyumba mwanu ndi mtima wangwiro.
3
Sindidzaika cinthu coipa pamaso panga; Cocita iwo akupatuka padera cindiipira; Sicidzandimamatira.
4
Mtima wopulukira udzandicokera; Sindidzadziwana naye woipa.
5
Wakuneneza mnzace m'tseri ndidzamdula; Wa maso odzikuza ndi mtima wodzitama sindidzamlola.
6
Maso anga ayang'ana okhulupirika m'dziko, kuti akhale ndi Ine; Iye amene ayenda m'njira yangwiro, iyeyu adzanditumikira Ine.
7
Wakucita cinyengo sadzakhala m'kati mwa nyumba yanga; Wakunena mabodza sadzakhazikika pamaso panga.
8
Mamawa onse ndidzadula oipa onse a m'dziko; Kuduliratu onse akucita zopanda pace ku mudzi wa Yehova.
Chewa Bible 1992
Zambia Bible Society, Malawi Bible Society and Zimbabwe Bible Society
:
Sungani Zolemba