Buku Loyera
|
| 1 |
| Ndidzaimba nyimbo zotamanda kukhulupirika ndi kulungama. Ndidzakuimbirani Inu Chauta. |
| 2 |
| Ndidzatsata njira yopanda cholakwa. Nanga mudzabwera liti kwa ine? Ndidzakhala ndi mtima wangwiro m'nyumba mwanga. |
| 3 |
| Sindidzaika maso anga pa chinthu chilichonse chachabechabe. Ndimadana ndi zochita za anthu okusiyani, sizindikomera konse. |
| 4 |
| Ndidzakhala kutali ndi anthu a mtima woipa, sindidzalola choipa chilichonse kuloŵa mwa ine. |
| 5 |
| Munthu wosinjirira mnzake kuseri ndidzamcheteketsa. Wooneka wonyada ndi wodzikuza sindidzamulekerera. |
| 6 |
| Koma anthu okhulupirika am'dziko, ndidzaŵayang'ana moŵakomera mtima, ndipo adzakhala ndi ine. Oyenda m'njira yopanda cholakwa adzanditumikira. |
| 7 |
| Palibe munthu wochita zonyenga amene adzakhale m'nyumba mwanga. Palibe munthu wolankhula zabodza amene adzakhale pafupi ndi ine. |
| 8 |
| Tsiku ndi tsiku ndidzaononga oipa onse am'dziko. Onse ochita zoipa ndidzaŵachotsa mu mzinda wa Chauta. |
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewablydc/psalms/101.mp3
150
101