|
| 1 |
|
| Lemekeza Yehova, moyo wanga; Ndi zonse za m'kati mwanga zilemekeze dzina lace loyera. |
|
| 2 |
|
| Lemekeza Yehova, moyo wanga, Ndi kusaiwala zokoma zace zonse aticitirazi: |
|
| 3 |
|
| Amene akhululukira mphulupulu zako zonse; Naciritsa nthenda zako zonse; |
|
| 4 |
|
| Amene aombola moyo wako ungaonongeke; Nakubveka korona wa cifundo ndi nsoni zokoma: |
|
| 5 |
|
| Amene akhutitsa m'kamwa mwako ndi zabwino; Nabweza ubwana wako unge mphungu. |
|
| 6 |
|
| Yehova acitira onse osautsidwa Cilungamo ndi ciweruzo. |
|
| 7 |
|
| Analangiza Mose njira zace, Ndi ana a Israyeli macitidwe ace. |
|
| 8 |
|
| Yehova ndiye wa nsoni zokoma ndi wacisomo, Wosakwiya msanga, ndi wa cifundo cocuruka. |
|
| 9 |
|
| Sadzatsutsana nao nthawi zanse; Ndipo sadzasunga mkwiyo wace kosatha. |
|
| 10 |
|
| Sanaticitira monga mwa zolakwa zathu, Kapena kutibwezera monga mwa mphulupulu zathu. |
|
| 11 |
|
| Pakuti monga m'mwamba mutalikira ndi dziko lapansi, Motero cifundo cace cikulira iwo akumuopa Iye. |
|
| 12 |
|
| Monga kum'mawa kutanimpha ndi kumadzulo, Momwemo anatisiyanitsira kutali zolakwa zathu. |
|
| 13 |
|
| Monga atate acitira ana ace cifundo, Yehova acitira cifundo iwo akumuopa Iye. |
|
| 14 |
|
| Popeza adziwa mapangidwe athu; Akumbukila kuti ife ndife pfumbi. |
|
| 15 |
|
| Koma munthu, masiku ace akunga udzu; Aphuka monga duwa la kuthengo. |
|
| 16 |
|
| Pakuti mphepo ikapitapo pakhala palibe: Ndi malo ace salidziwanso. |
|
| 17 |
|
| Koma cifundo ca Yehova ndico coyambira nthawi yosayamba kufikira nthawi yosatha kwa iwo akumuopa Iye, Ndi cilungamo cace kufikira kwa ana a ana; |
|
| 18 |
|
| Kwa iwo akusunga cipangano cace, Ndi kwa iwo akukumbukila malangizo ace kuwacita. |
|
| 19 |
|
| Yehova anakhazika mpando wacifumu wace Kumwamba; Ndi ufumu wace ucita mphamvu ponsepo, |
|
| 20 |
|
| Lemekezani Yehova, inu angelo ace; A mphamvu zolimba, akucita mau ace, Akumvera liu la mau ace. |
|
| 21 |
|
| Lemekezani Yehova, inu makamu ace onse; Inu atumiki ace akucita comkondweretsa Iye, |
|
| 22 |
|
| Lemekezani Yehova, inu, nchito zace zonse, Ponse ponse pali ufumu wace: Lemekeza Yehova, moyo wanga iwe. |
|
|
|
|