|
| 1 |
|
| Salimo la Davide. Tamanda Yehova, iwe moyo wanga; ndi zonse zamʼkati mwanga zitamande dzina lake loyera. |
|
| 2 |
|
| Tamanda Yehova, iwe moyo wanga, ndipo usayiwale zabwino zake zonse. |
|
| 3 |
|
| Amene amakhululuka machimo ako onse ndi kuchiritsa nthenda zako zonse, |
|
| 4 |
|
| amene awombola moyo wako ku dzenje ndi kukuveka chikondi ndi chifundo chake ngati chipewa chaufumu, |
|
| 5 |
|
| amene akwaniritsa zokhumba zako ndi zinthu zabwino, kotero kuti umakhala wamphamvu zatsopano ngati mphungu. |
|
| 6 |
|
| Yehova amachita chilungamo ndipo amaweruza molungama onse opsinjika. |
|
| 7 |
|
| Iye anadziwitsa Mose njira zake, ntchito zake kwa Aisraeli. |
|
| 8 |
|
| Yehova ndi wachifundo ndi wokoma mtima, wosakwiya msanga ndi wachikondi chochuluka. |
|
| 9 |
|
| Iye sadzatsutsa nthawi zonse, kapena kusunga mkwiyo wake kwamuyaya; |
|
| 10 |
|
| satichitira molingana ndi machimo athu, kapena kutibwezera molingana ndi mphulupulu zathu. |
|
| 11 |
|
| Pakuti monga kumwamba kuli kutali ndi dziko lapansi, koteronso chikondi chake nʼchachikulu kwa iwo amene amamuopa; |
|
| 12 |
|
| monga kummawa kutalikirana ndi kumadzulo, koteronso Iye watichotsera mphulupulu zathu kuti zikhale kutali nafe. |
|
| 13 |
|
| Monga bambo amachitira chifundo ana ake, choncho Yehova ali ndi chifundo ndi iwo amene amamuopa; |
|
| 14 |
|
| pakuti Iye amadziwa momwe tinawumbidwira, amakumbukira kuti ndife fumbi. |
|
| 15 |
|
| Kunena za munthu, masiku ake ali ngati udzu, amaphuka ngati duwa la mʼmunda; |
|
| 16 |
|
| koma mphepo imawombapo ndipo silionekanso ndipo malo ake sakumbukirikanso. |
|
| 17 |
|
| Koma kuchokera muyaya mpaka muyaya chikondi cha Yehova chili ndi iwo amene amamuopa, ndi chilungamo chake chili ndi ana a ana awo; |
|
| 18 |
|
| iwo amene amasunga pangano lake ndi kukumbukira kumvera malangizo ake. |
|
| 19 |
|
| Yehova wakhazikitsa mpando wake waufumu mmwamba ndipo ufumu wake umalamulira onse. |
|
| 20 |
|
| Tamandani Yehova, inu angelo ake, amphamvu inu amene mumachita zimene amalamula, amene mumamvera mawu ake. |
|
| 21 |
|
| Tamandani Yehova, zolengedwa zonse zakumwamba, inu atumiki ake amene mumachita chifuniro chake. |
|
| 22 |
|
| Tamandani Yehova, ntchito yake yonse kulikonse mu ulamuliro wake. Tamanda Yehova, iwe moyo wanga. |
|
|
|
|