|
| 1 |
|
| Yamikani Yehova, itanirani pa dzina lace; Bukitsani mwa mitundu ya anthu zocita Iye. |
|
| 2 |
|
| Myimbireni, myimbireni zomlemekeza; Fotokozerani zodabwiza zace zonse. |
|
| 3 |
|
| Mudzitamandire ndi dzina lace loyera: Mitima yao ya iwo ofunsira Yehova ikondwere. |
|
| 4 |
|
| Funani Yehova, ndi mphamvu yace; Funsirani nkhope yace nthawi zonse. |
|
| 5 |
|
| Kumbukilani zodabwiza zace adazicita; Zizindikilo zace ndi maweruzo a pakamwa pace; |
|
| 6 |
|
| Inu mbeu za Abrahamu, mtumiki wace, Inu ana a Yakobo, osankhika ace. |
|
| 7 |
|
| Iye ndiye Yehova, Mulungu wathu; Maweruzo ace akhala pa dziko lonse lapansi. |
|
| 8 |
|
| Akumbukila cipangano cace kosatha, Mauwo anawalamulira mibadwo zikwi; |
|
| 9 |
|
| Cipanganoco anapangana ndi Abrahamu, Ndi lumbiro lace ndi Isake; |
|
| 10 |
|
| Ndipo anaciimikira Yakobo, cikhale malemba, Cikhale cipangano cosatha kwa Israyeli. |
|
| 11 |
|
| Ndi kunena kuti, Ndidzakupatsa iwe dziko la Kanani, Gawo la colandira cako; |
|
| 12 |
|
| Pokhala iwo anthu owerengeka, Inde, anthu pang'ono, ndi alendo m'mwemo; |
|
| 13 |
|
| Nayendayenda kucokera mtundu wina kufikira mtundu wina, Kucokera ufumu wina kufikira anthu ena. |
|
| 14 |
|
| Sanalola munthu awasautse; Ndipo anadzudzula mafumu cifukwa ca iwowa; |
|
| 15 |
|
| Ndi kuti musamakhudza odzozedwa anga, Musamacitira coipa aneneri anga. |
|
| 16 |
|
| Ndipo anaitana njala igwere dziko; Anatyola mcirikizo wonse wa mkate. |
|
| 17 |
|
| Anawatsogozeratu munthu; Anamgulitsa Yosefe akhale kapolo: |
|
| 18 |
|
| Anapweteka miyendo yace ndi matangadza; Anamgoneka m'unyolo; |
|
| 19 |
|
| Kufikira nyengo yakucitika maneno ace; Mau a Yehova anamuyesa. |
|
| 20 |
|
| Mfumuyo anatuma munthu nammasula; Woweruza mitundu ya anthu anamtsegulira. |
|
| 21 |
|
| Anamuika akhale woyang'anira nyumba yace, Ndi woweruza wa pa zace zonse: |
|
| 22 |
|
| Amange nduna zace iye mwini, Alangize akulu ace adziwe nzeru. |
|
| 23 |
|
| Pamenepo Israyeli analowa m'Aigupto; Ndi Yakobo anakhala mlendo m'dziko la Hamu. |
|
| 24 |
|
| Ndipo anacurukitsatu mtundu wa anthu ace, Nawapatsa mphamvu yoposa owasautsa. |
|
| 25 |
|
| Anasanduliza mitima yao, kuti adane nao anthu ace, Kuti acite monyenga ndi atumiki ace. |
|
| 26 |
|
| Anatuma Mose mtumiki wace, Ndi Aroni amene adamsankha. |
|
| 27 |
|
| Anaika pakati pao zizindikilo zace, Ndi zodabwiza m'dziko la Hamu. |
|
| 28 |
|
| Anatumiza mdima ndipo kunada; Ndipo sanapikisana nao mau ace. |
|
| 29 |
|
| Anasanduliza madzi ao akhale mwazi, Naphanso nsomba zao. |
|
| 30 |
|
| Dziko lao linacuruka acule, M'zipinda zomwe za mafumu ao. |
|
| 31 |
|
| Ananena, ndipo inadza mitambo ya nchenche, Ndi nsabwe kufikira m'malire ao onse. |
|
| 32 |
|
| Anawapatsa mvula yamatalala, Lawi la moto m'dziko lao. |
|
| 33 |
|
| Ndipo anapanda mipesa yao, ndi mikuyu yao; Natyola mitengo kufikira m'malire ao onse. |
|
| 34 |
|
| Ananena, ndipo linadza dzombe Ndi mphuci, ndizo zosawerengeka, |
|
| 35 |
|
| Ndipo zinadya zitsamba zonse za m'dziko mwao, Zinadyanso zipatso za m'nthaka mwao. |
|
| 36 |
|
| Ndipo Iye anapha acisamba onse m'dziko mwao Coyambira ca mphamvu yao yonse. |
|
| 37 |
|
| Ndipo anawaturutsa pamodzi ndi siliva ndi golidi: Ndi mwa mafuko ao munalibe mmodzi wokhumudwa. |
|
| 38 |
|
| Aigupto anakondwera pakucoka iwo; Popeza kuopsa kwao kudawagwera. |
|
| 39 |
|
| Anayala mtambo uwaphimbe; Ndi moto uunikire usiku, |
|
| 40 |
|
| Anafunsa ndipo Iye anadzetsa zinziri. Nawakhuritsa mkate wakumwamba. |
|
| 41 |
|
| Anatsegula pathanthwe, anaturukamo madzi; Nayenda pouma ngati mtsinje. |
|
| 42 |
|
| Popeza anakumbukila mau ace oyera, Ndi Abrahamu mtumiki wace. |
|
| 43 |
|
| Potero anaturutsa anthu ace ndi kusekerera, Osankhika ace ndi kupfuula mokondwera. |
|
| 44 |
|
| Ndipo anawapatsa maiko a amitundu; Iwo ndipo analanda zipatso za nchito ya anthu: |
|
| 45 |
|
| Kuti asamalire malemba ace, Nasunge malamulo ace. Haleluya. |
|
|
: |
| 1 | | 2 | | 3 | | 4 | | 5 | | 6 | | 7 | | 8 | | 9 | | 10 | | 11 | | 12 | | 13 | | 14 | | 15 | | 16 | | 17 | | 18 | | 19 | | 20 | | 21 | | 22 | | 23 | | 24 | | 25 | | 26 | | 27 | | 28 | | 29 | | 30 | | 31 | | 32 | | 33 | | 34 | | 35 | | 36 | | 37 | | 38 | | 39 | | 40 | | 41 | | 42 | | 43 | | 44 | | 45 | 1
1
1 |
|
|---|
|
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa1992/psalms/105.mp3
150
105