×

Buku Lopatulika 1992

MASALIMO 108

1
Wakhazikika mtima wanga, Mulungu; Ndidzayimba, inde ndidzayimba zolemekeza, ndiko ulemerero wanga.
2
Galamukani, cisakasa ndi zeze; Ndidzauka ndekha mamawa.
3
Ndidzakuyamikani mwa mitundu ya anthu, Yehova: Ndipo ndidzayimba zakukulemekezani mwa anthu.
4
Pakuti cifundo canu ncacikuru kupitirira kumwamba, Ndi coonadi canu kufikira mitambo.
5
Kwezekani pamwamba pa thambo, Mulungu; Ndi ulemerero wanu pamwamba pa dziko lonse lapansi.
6
Kuti okondedwa anu alanditsidwe, Pulumutsani ndi dzanja lanu lamanja ndipo mutibvomereze.
7
Mulungu analankhula m'ciyero cace; ndidzakondwerera: Ndidzagawa Sekemu; ndidzayesa muyeso cigwa ca Sukoti.
8
Gileadi ndi wanga: Manase ndi wanga; Ndi Efraimu ndiye mphamvu ya mutu wanga; Yuda ndiye wolamulira wanga.
9
Moabu ndiye mkhate wanga; Pa Edomu ndidzaponya nsapato yanga; Ndidzapfuulira Filistiya,
10
Adzandifikitsa ndani m'mudzi wa m'linga? Adzanditsogolera ndani ku Edomu?
11
Si ndinu Mulungu, amene mwatitaya Osaturuka nao magulu athu?
12
Tithandizeni mumsauko; Pakuti cipulumutso ca munthu ndi cabe.
13
Mwa Mulungu tidzacita molimbika mtima: Ndipo Iye adzapondereza otisautsa.
Chewa Bible 1992
Zambia Bible Society, Malawi Bible Society and Zimbabwe Bible Society
:
Sungani Zolemba