×

Buku Loyera

MASALIMO 108

1
Inu Mulungu, mtima wanga wakonzeka, ndithu, mtima wanga wakonzekadi! Ndidzaimba nyimbo, nyimbo yake yotamanda. Lumpha, iwe mtima wanga.
2
Inu zeze ndi pangwe, tiyeni lirani. Ndidzadzutsa dzuŵa ndi nyimbo zanga.
3
Ndidzakuthokozani, Inu Chauta, pakati pa mitundu ya anthu. Ndidzaimba nyimbo zokutamandani pakati pa anthu a m'maiko onse,
4
pakuti chikondi chanu chosasinthika nchachikulu, chofika mpaka pamwamba pa mlengalenga, kukhulupirika kwanu kumafika mpaka ku mitambo.
5
Inu Mulungu, onetsani ukulu wanu mumlengalenga monse. Wanditsani ulemerero wanu pa dziko lonse lapansi.
6
Tipambanitseni pa nkhondo ndi dzanja lanu lamanja, mundiyankhe kuti ife, okondedwa anu, tipulumuke.
7
Mulungu ali ku malo ake oyera, walonjeza kuti, “Ndidzakugaŵirani dziko la Sekemu mokondwa, ndidzakulemberani malire m'chigwa cha Sukoti.
8
“Giliyadi ndi wanga, Manase ndi wanga. Efuremu ali ngati chisoti changa chodzitetezera. Yuda ali ngati ndodo yanga yaufumu.
9
“Mowabu adzakhala ngati mbale yosambiramo ine. Edomu adzakhala poponda nsapato zanga. Ndidzafuula mokondwa nditagonjetsa Filistiya.”
10
Ndani adzandifikitse ku mzinda wamalinga? Ndani adzanditsogolere ku Edomu?
11
Si wina ai koma ndinu Mulungu amene mwatitaya, ndinu Mulungu amene mwaleka kuperekeza ankhondo athu.
12
Tithandizeni kulimbana ndi adani athuwo, pakuti chithandizo cha munthu nchopandapake.
13
Mulungu akakhala nafe, tidzamenya nkhondo molimba mtima, pakuti ndiye amene adzapondereza adani athu.
Chewa Bible BLYDC
Bible Society of Malawi
:
Sungani Zolemba