×

Buku Loyera

MASALIMO 109

1
Musakhale chete, Inu Mulungu, amene ndimakutamandani,
2
pakuti anthu oipa ndi onama amakamba zondiwukira, amalankhula zondinamizira.
3
Ponseponse amandilankhula mau achidani, amandinena popanda chifukwa.
4
M'malo mwa chikondi changa, iwo amandibwezera zondineneza, ngakhale pamene ndikuŵapempherera.
5
Motero amandibwezera zoipa m'malo mwa zabwino, amandiwonetsa chidani m'malo mwa chikondi changa.
6
Sankhulani munthu woipa kuti aweruze mlandu wa wondiwukirayo, iye aimbidwe mlandu ndi munthu woneneza anzake.
7
Pomuweruza apezeke kuti ali ndi mlandu, mapemphero ake akhale ngati kupalamula.
8
Masiku ake akhale oŵerengeka, wina alandire udindo wake.
9
Ana ake akhale amasiye, ndipo mkazi wake akhale mfedwa.
10
Ana ake azingoyendayenda nkumapemphapempha, apirikitsidwe m'mabwinja m'mene amakhala.
11
Wokongoza ndalama amlande zonse zimene ali nazo. Alendo afunkhe zimene adapindula ndi ntchito yake.
12
Pasapezeke ndi mmodzi yemwe womukomera mtima, kapena wina woŵachitira chifundo ana ake amasiye aja.
13
Zidzukulu zake zithe nkufa, dzina lao lisamvekenso mu mbadwo wachiŵiri.
14
Chauta asaiŵale machimo a makolo ake, machimo a mai wake asafafanizike.
15
Chauta asakhululukire machimowo mpaka muyaya, anthuwo aiŵalike pa dziko lapansi.
16
Pakuti munthuyo sadakumbukire kuchita chifundo, koma adazunza osauka, osoŵa ndi ovutika mu mtima, mpaka kuŵapha.
17
Ankakonda kutemberera, choncho matemberero amgwere. Sadakonde kudalitsa anthu ena, choncho madalitso akhale kutali ndi iye.
18
Kutemberera anzake kunali ngati chovala chake, motero matemberero amgwere ngati mvula. Akhale ngati mafuta oloŵa m'mafupa mwake.
19
Matemberero akhale ngati mwinjiro wofundira, ngati lamba wovala tsiku ndi tsiku.
20
Zimenezi zikhale chilango chochokera kwa Chauta kugwera ondineneza. Ziŵagwere amene amalankhula zoipira moyo wanga.
21
Koma Inu Mulungu, Ambuye anga, munditchinjirize malinga ndi ulemerero wa dzina lanu, mundipulumutse chifukwa chikondi chanu chosasinthika ndi chabwino.
22
Pakuti ine ndine wosauka ndi wosoŵa, ndipo mtima wanga ukuŵaŵa kwambiri.
23
Ndazimirira ngati mthunzi wamadzulo, ndapirikitsidwa ngati dzombe.
24
Maondo anga afooka chifukwa chosala zakudya, thupi langa laonda ndi mutu womwe.
25
Ondineneza amandinyodola, akandiwona amapukusa mitu yao.
26
Thandizeni Chauta, Mulungu wanga. Pulumutseni chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika.
27
Adani adziŵe kuti limeneli ndi dzanja lanu londipulumutsa, Inu Chauta, ndinu amene mwachita zimenezi.
28
Iwo atemberere, koma Inu mundidalitse. Ondiputa muŵachititse manyazi, koma ine mtumiki wanu ndisangalale.
29
Ondineneza akhale onyozeka, manyazi ao aŵakute ngati chovala.
30
Ndidzathokoza Chauta kwambiri polankhula. Ndidzamtamanda pakati pa gulu la anthu.
31
Paja Chauta amaimirira pafupi ndi munthu wosoŵa, amafuna kumpulumutsa kwa anthu ogamula kuti iyeyo aphedwe.
Chewa Bible BLYDC
Bible Society of Malawi
:
Sungani Zolemba