Buku Lopatulika 1992
|
| 1 |
| Ndakhulupirira Yehova: Mutani nkunena kwa moyo wanga, Thawirani ku phiri lanu ngati mbalame? |
| 2 |
| Pakuti, onani, oipa akoka uta, Apiringidza mubvi wao pansinga, Kuwaponyera mumdima oongoka mtima. |
| 3 |
| Akapasuka maziko, Wolungama angacitenji? |
| 4 |
| Yehova ali m'Kacisi wace woyera, Yehova, mpando wacifumu wace uli m'Mwamba; Apenyerera ndi maso ace, ayesa ana a anthu ndi zikope zace. |
| 5 |
| Yehova ayesa wolungama mtima: Koma moyo wace umuda woipa ndi iye wakukonda ciwawa. |
| 6 |
| Adzagwetsa pwata pwata misampha pa oipa; Moto ndi miyala yasuifure, ndi mphepo yoopsa zidzawagawikira m'cikho cao. |
| 7 |
| Pakuti Yehova ndiye wolungama; akonda zolungama: Woongoka mtima adzapenya nkhope yace. |
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa1992/psalms/011.mp3
150
11