Mawu a Mulungu 2016
|
| 1 |
| Salimo la Davide. Yehova akuwuza Mbuye wanga kuti, “Khala ku dzanja langa lamanja mpaka nditasandutsa adani ako kukhala chopondapo mapazi ako.” |
| 2 |
| Yehova adzakuza ndodo yamphamvu ya ufumu wako kuchokera mʼZiyoni; udzalamulira pakati pa adani ako. |
| 3 |
| Ankhondo ako adzakhala odzipereka pa tsiku lako la nkhondo. Atavala chiyero chaulemerero, kuchokera mʼmimba ya mʼbandakucha, udzalandira mame a unyamata wako. |
| 4 |
| Yehova walumbira ndipo sadzasintha maganizo ake: “Ndiwe wansembe mpaka muyaya monga mwa unsembe wa Melikizedeki.” |
| 5 |
| Ambuye ali kudzanja lako lamanja; Iye adzaponda mafumu pa tsiku la ukali wake. |
| 6 |
| Adzaweruza anthu a mitundu ina, adzadzaza dziko lapansi ndi mitembo ndipo adzaphwanya olamulira a pa dziko lonse lapansi. |
| 7 |
| Iye adzamwa mu mtsinje wa mʼmbali mwa njira; choncho adzaweramutsa mutu wake. |
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2016/psalms/110.mp3
150
110