Buku Loyera
|
| 1 |
| Chauta adauza Mbuye wanga kuti, “Khala ku dzanja langa lamanja, mpaka nditasandutsa adani ako kukhala ngati chopondapo mapazi ako.” |
| 2 |
| Chauta adzakuza ufumu wako wamphamvu kuchokera ku Ziyoni. Adzati, “Khala mfumu yolamulira adani ako.” |
| 3 |
| Anthu ako adzadzipereka mwaufulu, pa tsiku limene udzaonetse mphamvu zako pa phiri loyera. Anyamata ako adzabwera kwa iwe mu unyinji wao, monga m'mene mame amabwerera m'mamaŵa. |
| 4 |
| Chauta walumbira ndipo sadzasintha maganizo ake akuti, “Ndiwe wansembe mpaka muyaya, unsembe wake wonga uja wa Melkizedeki.” |
| 5 |
| Ambuye ali pambali pako. Adzaphwanya mafumu pa tsiku la mkwiyo wao. |
| 6 |
| Adzalanga mitundu ya anthu akunja, adzadzaza dziko lapansi ndi mitembo. Adzagonjetsa olamulira a pa dziko lonse lapansi. |
| 7 |
| Adzamwa mu mtsinje wam'njira, ndipo adzaŵeramutsa mutu monyadira. |
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewablydc/psalms/110.mp3
150
110