Buku Lopatulika 1992
|
| 1 |
| Haleluya; Lemekezani, inu atumiki a Yehova; Lemekezani dzina la Yehova, |
| 2 |
| Lodala dzina la Yehova. Kuyambira tsopano kufikira kosatha. |
| 3 |
| Citurukire dzuwa kufikira kulowa kwace Lilemekezedwe dzina la Yehova. |
| 4 |
| Yehova akwezeka pamwamba pa amitundu onse, Ulemerero wace pamwambamwamba. |
| 5 |
| Akunga Yehova Mulungu wathu ndani? Amene akhala pamwamba patali, |
| 6 |
| Nadzicepetsa apenye Zam'mwamba ndi za pa dziko lapansi. |
| 7 |
| Amene autsa wosauka lrumcotsa kupfumbi, Nakweza waumphawi kumcotsa kudzala. |
| 8 |
| Kuti amkhalitse pamodzi ndi akulu, Pamodzi ndi akulu a anthu ace. |
| 9 |
| Asungitsa nyumba mkazi wosaonamwana, Akhale mai wokondwera ndi ana. Haleluya. |
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa1992/psalms/113.mp3
150
113