Buku Loyera
|
| 1 |
| Tamandani Chauta! Mtamandeni, inu atumiki ake, tamandani dzina la Chauta. |
| 2 |
| Yamikani Chauta kuyambira tsopano mpaka muyaya. |
| 3 |
| Dzina la Chauta litamandike kuyambira ku matulukiro a dzuŵa mpaka ku maloŵero ake. |
| 4 |
| Chauta akulamulira anthu a mitundu yonse, ulemerero wake ndi waukulu kuposa wa mlengalenga. |
| 5 |
| Ndani angalingane ndi Chauta, Mulungu wathu, amene akukhala kumwamba, |
| 6 |
| wochita kuŵeramira pansi poyang'ana mlengalenga ndi dziko lapansi. |
| 7 |
| Amakweza munthu wosauka kuchokera ku fumbi, ndipo amatulutsa ku dzala anthu osoŵa. |
| 8 |
| Amaŵakhazika pamodzi ndi mafumu, mafumu a anthu a Chauta. |
| 9 |
| Amapatsa banja mkazi wosabala, namsandutsa mai wosangalala wa ana. Tamandani Chauta! |
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewablydc/psalms/113.mp3
150
113