Buku Lopatulika 1992
|
| 1 |
| M'mene Israyeli anaturuka ku Aigupto, Nyumba ya Yakobo kwa anthu a cinenedwe cacilendo; |
| 2 |
| Yuda anakhala malo ace oyera, Israyeli ufumu wace. |
| 3 |
| Nyanjayo inaona, nithawa; Yordano anabwerera m'mbuyo. |
| 4 |
| Mapiri anatumphatumpha ngati nkhosa zamphongo, Timapiri ngati ana a nkhosa. |
| 5 |
| Unathawanji nawe, nyanja iwe? Unabwerereranji m'mbuyo, Yordano iwe? |
| 6 |
| Munatumpha-tumphiranji ngati nkhosa zamphongo, mapiri inu? Ngati ana a nkhosa, zitunda inu? |
| 7 |
| Unjenjemere, dziko lapansi iwe, pamaso pa Ambuye, Pamaso pa Mulungu wa Yakobo; |
| 8 |
| Amene anasanduliza thanthwe likhale thawale lamadzi, Nsangalabwi ikhale kasupe wamadzi. |
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa1992/psalms/114.mp3
150
114