Buku Lopatulika 1992
|
| 1 |
| Kwa ife ai, Yehova, kwa ife ai, Koma kwa dzina lanu patsani ulemerero, Cifukwa ca cifundo canu, ndi coonadi canu. |
| 2 |
| Aneneranji amitundu, Ali kuti Mulungu wao? |
| 3 |
| Koma Mulungu wathu ndiye ali m'mwamba; Acita ciri conse cimkonda. |
| 4 |
| Mafano ao ndiwo a siliva ndi golidi, Nchito za manja a anthu. |
| 5 |
| Pakamwa ali napo, koma osalankhula; Maso ali nao, koma osapenya; |
| 6 |
| Makutu ali nao, koma osamva; Mphuno ali nazo, koma osanunkhiza; |
| 7 |
| Manja ali nao, koma osagwira; Mapazi ali nao, koma osayenda; Kapena sanena pammero pao, |
| 8 |
| Adzafanana nao iwo akuwapanga; Ndi onse akuwakhulupirira, |
| 9 |
| Israyeli, khulupirira Yehova: Ndiye mthandizi wao ndi cikopa cao. |
| 10 |
| Nyumba ya Aroni, khulupirira Yehova: Ndiye mthandizi wao, ndi cikopa cao. |
| 11 |
| Inu akuopa Yehova, khulupirirani Yehova; Ndiye mthandizi wao ndi cikopa cao. |
| 12 |
| Yehova watikumbukila; adzatidalitsa: Adzadalitsa nyumba ya Israyeli; Adzadalitsa nyumba ya Aroni. |
| 13 |
| Adzadalitsa iwo akuopa Yehova, Ang'ono ndi akuru. |
| 14 |
| Yehova akuonjezereni dalitso, Inu ndi ana anu. |
| 15 |
| Odalitsika inu a kwa Yehova, Wakulenga kumwamba ndi dziko lapansi. |
| 16 |
| Kunena za kumwamba, kumwamba ndiko kwa Yehova; Koma dziko lapansi analipereka kwa ana a anthu. |
| 17 |
| Akufa salemekeza Yehova, Kapena ali yense wakutsikira kuli cete: |
| 18 |
| Koma ife tidzalemekeza Yehova Kuyambira tsopano kufikira nthawi yonse. Haleluya. |
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa1992/psalms/115.mp3
150
115