Buku Lopatulika 1992
|
| 1 |
| Ndimkonda, popeza Yehova amamva, Mau anga ndi kupemba kwanga. |
| 2 |
| Popeza amandicherera khutu lace, Cifukwa cace ndidzaitanira Iye masiku anga onse. |
| 3 |
| Zingwe za imfa zinandizinga, Ndi zowawa za manda zinandigwira: Ndinapeza nsautso ndi cisoni. |
| 4 |
| Pamenepo ndinaitana dzina la Yehova; Ndikuti, Yehova ndikupemphani landitsani moyo wanga. |
| 5 |
| Yehova ngwa cifundo ndi wolungama; Ndi Mulungu wathu ngwa nsoni. |
| 6 |
| Yehova asunga opusa; Ndidafoka ine, koma anandipulumutsa, |
| 7 |
| Ubwere moyo wanga ku mpumulo wako; Pakuti Yehova anakucitira cokoma. |
| 8 |
| Pakuti munalanditsa moyo wanga kuimfa, Maso anga kumisozi, Mapazi anga, ndingagwe. |
| 9 |
| Ndidzayenda pamaso pa Yehova M'dziko la amoyo. |
| 10 |
| Ndinakhulupirira, cifukwa cace ndinalankhula; Ndinazunzika kwambiri. |
| 11 |
| Pofulumizidwa mtima ndinati ine, Anthu Onse nga mabodza. |
| 12 |
| Ndidzabwezera Yehova ciani Cifukwa ca zokoma zace zonse anandicitira? |
| 13 |
| Ndidzanyamula cikho ca cipulumutso, Ndipo ndidzaitanira dzina la Yehova, |
| 14 |
| Ndidzacitazowindazanga za kwa Yehova, Tsopano, pamaso pa anthu ace onse. |
| 15 |
| Imfa ya okondedwa ace Nja mtengo wace pamaso pa Yehova. |
| 16 |
| Ndiloleni, Yehova, indetu ndine mtumiki wanu; Ndine mtumiki wanu, mwana wa mdzakazi wanu; Mwandimasulira zondimanga, |
| 17 |
| Ndidzapereka kwa Inu nsembe yaciyamiko, Ndipo ndidzaitanira dzina la Yehova. |
| 18 |
| Ndidzacita zowinda zanga za kwa Yehova, Tsopano, pamaso pa anthu ace onse; |
| 19 |
| M'mabwalo a nyumba ya Yehova, Pakati pa inu, Yerusalemu. Haleluya. |
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa1992/psalms/116.mp3
150
116