Mawu a Mulungu 2016
|
| 1 |
| Ndimakonda Yehova pakuti Iyeyo amamva mawu anga; Iye amamva kulira kwanga kopempha chifundo. |
| 2 |
| Pakuti ananditchera khutu, ndidzayitana Iye masiku onse a moyo wanga. |
| 3 |
| Zingwe za imfa zinandizinga, zoopsa za ku dziko la anthu akufa zinandigwera; ndinapeza mavuto ndi chisoni. |
| 4 |
| Pamenepo ndinayitana dzina la Yehova: “Inu Yehova, pulumutseni!” |
| 5 |
| Yehova ndi wokoma mtima ndi wolungama Mulungu wathu ndi wodzaza ndi chifundo. |
| 6 |
| Yehova amateteza munthu wodzichepetsa mtima; pamene ndinali ndi chosowa chachikulu, Iye anandipulumutsa. |
| 7 |
| Pumula iwe moyo wanga, pakuti Yehova wakuchitira zokoma. |
| 8 |
| Pakuti Inu Yehova mwapulumutsa moyo wanga ku imfa, maso anga ku misozi, mapazi anga kuti angapunthwe, |
| 9 |
| kuti ine ndiyende pamaso pa Yehova mʼdziko la anthu amoyo. |
| 10 |
| Ine ndinakhulupirira; choncho ndinati, “Ndasautsidwa kwambiri.” |
| 11 |
| Ndipo ndili mʼnkhawa yanga ndinati, “Anthu onse ndi abodza.” |
| 12 |
| Ndingamubwezere chiyani Yehova, chifukwa cha zokoma zake zonse zimene wandichitira? |
| 13 |
| Ndidzakweza chikho cha chipulumutso ndipo ndidzayitana dzina la Yehova. |
| 14 |
| Ndidzakwaniritsa malonjezo anga kwa Yehova pamaso pa anthu ake onse. |
| 15 |
| Imfa ya anthu oyera mtima ndi yamtengowapatali pamaso pa Yehova. |
| 16 |
| Inu Yehova, zoonadi ndine mtumiki wanu: ndine mtumiki wanu, mwana wa mdzakazi wanu; Inu mwamasula maunyolo anga. |
| 17 |
| Ndidzapereka nsembe yachiyamiko kwa Inu ndipo ndidzayitanira pa dzina la Yehova. |
| 18 |
| Ndidzakwaniritsa malonjezo anga kwa Yehova pamaso pa anthu ake onse, |
| 19 |
| mʼmabwalo a nyumba ya Yehova, mʼkati mwako iwe Yerusalemu. Tamandani Yehova. |
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2016/psalms/116.mp3
150
116