×

Buku Lopatulika 1922

MASALIMO 118

1
Yamikani Yehova; pakuti Iye ndiye wabwino; pakuti chifundo chake nchosatha.
2
Anene tsono Israele, kuti chifundo chake nchosatha.
3
Anene tsono nyumba ya Aroni, kuti chifundo chake nchosatha.
4
Anene tsono iwo akuopa Yehova, kuti chifundo chake nchosatha.
5
M'mene ndinasautsika ndinaitanira pa Yehova; anandiyankha nandiika motakasuka Yehova.
6
Yehova ndi wanga; sindidzaopa; adzandichitanji munthu?
7
Yehova ndi wanga, mwa iwo akundithandiza; m'mwemo ndidzaona chofuna ine pa iwo akundida.
8
Kuthawira kwa Yehova nkokoma koposa kukhulupirira munthu.
9
Kuthawira kwa Yehova nkokoma koposa kukhulupirira akulu.
10
Amitundu onse adandizinga, zedi, m'dzina la Yehova ndidzawaduladula.
11
Adandizinga, inde, adandizinga: Indedi, m'dzina la Yehova ndidzawaduladula.
12
Adandizinga ngati njuchi; anazima ngati moto waminga; indedi, m'dzina la Yehova ndidzawaduladula.
13
Kundikankha anandikankha ndikadagwa; koma Yehova anandithandiza.
14
Yehova ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga; ndipo anakhala chipulumutso changa.
15
M'mahema a olungama muli liu lakufuula mokondwera Dzanja lamanja la Yehova ndi la chipulumutso:
16
Dzanja lamanja la Yehova likwezeka, Dzanja lamanja la Yehova lichita mwamphamvu.
17
Sindidzafa koma ndidzakhala ndi moyo, ndipo ndidzafotokozera ntchito za Yehova.
18
Kulanga anandilangadi Yehova: koma sanandipereke kuimfa ai.
19
Nditsegulireni zipata za chilungamo; ndidzalowamo, ndidzayamika Yehova.
20
Chipata cha Yehova ndi ichi; olungama adzalowamo.
21
Ndidzakuyamikani, popeza munandiyankha, ndipo munakhala chipulumutso changa.
22
Mwala umene omangawo anaukana wakhala mutu wa pangodya.
23
Ichi chidzera kwa Yehova; nchodabwitsa ichi pamaso pathu.
24
Tsiku ili ndilo adaliika Yehova; tidzasekera ndi kukondwera m'mwemo.
25
Tikupemphani, Yehova, tipulumutseni tsopano; tikupemphani, Yehova, tipindulitseni tsopano.
26
Wodala wakudzayo m'dzina la Yehova; takudalitsani kochokera m'nyumba ya Yehova.
27
Yehova ndiye Mulungu, amene anatiunikira; mangani nsembe ndi zingwe, kunyanga za guwa la nsembe.
28
Inu ndinu Mulungu wanga, ndipo ndidzakuyamikani; ndinu Mulungu wanga, ndidzakukwezani.
29
Yamikani Yehova, pakuti Iye ndiye wabwino, pakuti chifundo chake nchosatha.
Chewa Bible 1922
Bible Society of Malawi
:
Sungani Zolemba