Buku Lopatulika 1992
|
| 1 |
| Pulumutsani, Yehova; pakuti wofatsa wasowa; Pakuti okhulupirika acepa mwa ana a anthu. |
| 2 |
| Amanena za bodza munthu yense ndi mnansi wace: Amanena ndi mlomo wotyasika, ndi mitima iwiri. |
| 3 |
| Yehova adzadula milomo yonse yotyasika, Lilime lakudzitamandira: |
| 4 |
| Amene amati, Ndi lilime lathu tidzaposa; Milomo yathu nja ife eni; mbuye wa pa ife ndani? |
| 5 |
| Cifukwa ca kupasuka kwa ozunzika, cifukwa ca kuusa moyo kwa aumphawi, Ndiuka tsopano, ati Yehova; Ndidzamlonga mosungika muja alaka-lakamo. |
| 6 |
| Mau a Yehova ndi mau oona; Ngati siliva woyenga m'ng'anjo yadothi, Yoiyeretsa kasanu ndi kawiri. |
| 7 |
| Mudzawasunga, Yehova, Mudzawacinjirizira mbadwo uno ku nthawi zonse. |
| 8 |
| Oipa amayenda mozungulira-zungulira, Potamanda iwo conyansa mwa ana a anthu. |
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa1992/psalms/012.mp3
150
12