Buku Lopatulika 1922
|
| 1 |
| Nyimbo yokwerera. Ndikweza maso anga kwa Inu, kwa Inu wakukhala kumwamba. |
| 2 |
| Taonani, monga maso a anyamata ayang'anira dzanja la mbuye wao, monga maso a adzakazi ayang'anira dzanja la mbuye wao wamkazi: Momwemo maso athu ayang'anira Yehova Mulungu wathu, kufikira atichitira chifundo. |
| 3 |
| Mutichitire chifundo, Yehova, mutichitire chifundo; pakuti takhuta kwambiri ndi mnyozo. |
| 4 |
| Moyo wathu wakhuta ndithu ndi kuseka kwa iwo osasowa kanthu, ndi mnyozo wa odzikuza. |
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2014/psalms/123.mp3
150
123