Buku Loyera
|
| 1 |
| Chauta akadapanda kukhala pa mbali yathu, Israele anene choncho tsopano, |
| 2 |
| Chauta akadapanda kukhala pa mbali yathu, pamene anthu adatiwukira, |
| 3 |
| bwenzi atatimeza amoyo, muja mkwiyo wao udatiyakira, |
| 4 |
| bwenzi chigumula chitatisesa, madzi amkokomo atatikokolola, |
| 5 |
| bwenzi madzi amphamvu atatimiza. |
| 6 |
| Atamandike Chauta, amene sadatipereke kwa anthuwo kuti atiwononge. |
| 7 |
| Taonjoka ngati mbalame mu msampha wa osaka, msampha wathyoka, ndipo ife tapulumuka. |
| 8 |
| Chithandizo chathu chimachokera kwa Chauta, amene adalenga kumwamba ndi dziko lapansi. |
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewablydc/psalms/124.mp3
150
124