Buku Lopatulika 1992
|
| 1 |
| Iwo akukhulupirira Yehova Akunga phiri la Ziyoni, losasunthika, likhazikika kosatha, |
| 2 |
| Monga mapiri azinga Yerusalemu, Momwemo Yehova azinga anthu ace, Kuyambira tsopano kufikira nthawi zonse. |
| 3 |
| Pakuti ndodo yacifumu ya coipa siidzapumula pa gawo la olungama; Kuti olungama asaturutse dzanja lao kucita cosalungama, |
| 4 |
| Citirani cokoma, Yehova, iwo okhala okoma; Iwo okhala oongoka mumtima mwao. |
| 5 |
| Koma iwo akupatuka kutsata njira zao zokhotakhota, Yehova adzawacotsa pamodzi ndi ocita zopanda pace. Mtendere ukhale pa Israyeli. |
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa1992/psalms/125.mp3
150
125