×

Buku Lopatulika 1992

MASALIMO 126

1
Pobweza Yehova ukapolo wa Ziyoni, Tinakhala ngati anthu akulota.
2
Pamenepo pakamwa pathu panadzala ndi kuseka, Ndi lilime lathu linapfuula mokondwera; Pamenepo anati mwa amitundu, Yehova anawacitira iwo zazikuru,
3
Yehova anaticitira ife zazikuru; Potero tikhala okondwera.
4
Bwezani ukapolo wathu, Yehova, Ngati mitsinje ya ku Mwera.
5
Akubzala ndi misozi adzatuta ndi kupfuula mokondwera.
6
Iye amene ayendayenda nalira, ponyamula mbeu yakufesa; Adzabweranso ndithu ndi kupfuula mokondwera, alikunyamula mitolo yace.
Chewa Bible 1992
Zambia Bible Society, Malawi Bible Society and Zimbabwe Bible Society
:
Sungani Zolemba