×

Buku Lopatulika 1992

MASALIMO 127

1
Akapanda kumanga nyumba Yehova, Akuimanga agwiritsa nchito cabe; Akapanda kusunga mudzi Yehoya, Mlonda adikira cabe.
2
Kuli cabe kwa inu Rulawirira mamawa ndi kusagonerapo madzulo, Kudya mkate wosautsa kuupeza; Kuli tero kuti izi apatsa okondedwa ace ngati m'tulo.
3
Taonani ana ndiwo colandira ca kwa Yehova; Cipatso ca m'mimba ndico mphotho yace.
4
Ana a ubwana wace wa munthu Akunga mibvi m'dzanja lace la ciphona.
5
Wodala munthu amene anadzaza nayo phodo lace: Sadzacita manyazi iwo, Pakulankhula nao adani kucipata.
Chewa Bible 1992
Zambia Bible Society, Malawi Bible Society and Zimbabwe Bible Society
:
Sungani Zolemba