×

Buku Loyera

MASALIMO 129

1
“Adani akhala akundizunza kwambiri kuyambira unyamata wanga,” Israele anene choncho tsopano,
2
“Adani akhala akundizunza kwambiri kuyambira unyamata wanga, komabe sadandipambane.
3
“Pondikwapula adani anga adachita ngati kulima pamsana panga, kulima mizere yaitali.”
4
Koma Chauta ndi wolungama, wandimasula zingwe za anthu oipa.
5
Anthu onse odana ndi Ziyoni agonjetsedwe ndi kupirikitsidwa mwamanyazi.
6
Akhale ngati udzu womera pa denga la nyumba, umene umafota usanakule.
7
Woumweta sangadzaze nkumanja komwe, womanga mitolo sangamange nchitsakato chomwe.
8
Anthu odutsapo sadzanena kwa omwetawo kuti, “Madalitso a Chauta akhale nanu.” “Tikukudalitsani potchula dzina la Chauta.”
Chewa Bible BLYDC
Bible Society of Malawi
:
Sungani Zolemba