Buku Lopatulika 1992
|
| 1 |
| Mudzandiiwala ciiwalire, Yehova, kufikira liti? Mudzandibisira ine nkhope yanu kufikira liti? |
| 2 |
| Ndidzacita uphungu m'moyo mwanga kufikira liti, Pokhala ndi cisoni m'mtima mwanga tsiku lonse? Adzandiukira ine mdani wanga kufikira liti? |
| 3 |
| Penyani, ndiyankheni, Yehova Mulungu wanga: Penyetsani maso anga, kuti ndingagone tulo ta imfa; |
| 4 |
| Kuti anganene mdani wanga, Ndamlaka; Ndipo angakondwere otsutsana nane posunthika ine. |
| 5 |
| Koma ine ndakhulupira pa cifundo canu; Mtima wanga udzakondwera naco cipulumutso canu: |
| 6 |
| Ndidzayimbira Yehova, Pakuti anandicitira zokoma. |
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa1992/psalms/013.mp3
150
13