Buku Loyera
|
| 1 |
| Ndikulirira Inu Chauta, ndili m'dzenje lozama lamavuto. |
| 2 |
| Ambuye imvani liwu langa. Tcherani khutu kuti mumve kupemba kwanga. |
| 3 |
| Inu Chauta, mukadaŵerengera machimo, ndani akadakhala chilili opanda mlandu, Ambuye? |
| 4 |
| Koma inu mumakhululukira, nchifukwa chake timakulemekezani. |
| 5 |
| Ndimayembekeza chithandizo cha Chauta, ndimayembekeza ndi mtima wonse, ndipo ndimakhulupirira mau ake. |
| 6 |
| Mtima wanga umayembekeza Chauta kupambana m'mene alonda amayembekezera mbandakucha, kupambanadi m'mene alonda amayembekezera mbandakucha. |
| 7 |
| Iwe Israele, khulupirira Chauta. Paja Chauta ndi wa chikondi chosasinthika, ndi wokonzeka kupulumutsa. |
| 8 |
| Adzaombola Israele ku machimo ake onse. |
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewablydc/psalms/130.mp3
150
130