|
| 1 |
|
| Haleluya; Lemekezani dzina la Yehova; Lemekezani inu atumiki a Yehova: |
|
| 2 |
|
| Inu akuimirira m'nyumba ya Yehova, M'mabwalo a nyumba ya Mulungu wathu. |
|
| 3 |
|
| Lemekezani Yehova; pakuti Yehova ndiye wabwino; Muyimbire zolemekeza dzina lace; pakuti nkokondweretsa kutero. |
|
| 4 |
|
| Pakuti Yehova anadzisankhira Yakobo, Israyeli, akhale cuma cace ceni ceni. |
|
| 5 |
|
| Pakuti ndidziwa kuti Yehova ndi wamkuru, Ndi Ambuye wathu aposa milungu yonse. |
|
| 6 |
|
| Ciri conse cimkonda Yehova acicita, Kumwamba ndi pa dziko lapansi, m'nyanja ndi mozama monse. |
|
| 7 |
|
| Akweza mitambo icokere ku malekezero a dziko lapansi; Ang'animitsa mphezi zidzetse mvula; Aturutsa mphepo mosungira mwace. |
|
| 8 |
|
| Anapanda oyamba a Aigupto, Kuyambira munthu kufikira zoweta. |
|
| 9 |
|
| Anatumiza zizindikilo ndi zodabwiza pakati pako, Aigupto iwe, Pa Farao ndi pa omtumikira onse. |
|
| 10 |
|
| Ndiye amene anapanda amitundu ambiri. Napha mafumu amphamvu; |
|
| 11 |
|
| Sihoni mfumu ya Aamori, Ndi Ogi mfumu ya Basana, Ndi maufumu onse a Kanani: |
|
| 12 |
|
| Ndipo anapereka dziko lao likhale cosiyira, Cosiyira ca kwa Israyeli anthu ace. |
|
| 13 |
|
| Dzina lanu, Yehova, likhala kosatha; Cikumbukilo canu, Yehova, kufikira mibadwo mibadwo. |
|
| 14 |
|
| Pakuti Yehova adzaweruza anthu ace, Koma adzaleka atumiki ace. |
|
| 15 |
|
| Mafano a amitundu ndiwo siliva ndi golidi, Nchito ya manja a anthu. |
|
| 16 |
|
| Pakamwa ali napo koma osalankhula; Maso ali nao, koma osapenya; |
|
| 17 |
|
| Makutu ali nao, koma osamva; Inde, pakamwa pao palibe mpweya. |
|
| 18 |
|
| Akuwapanga adzafanana nao; Inde, onse akuwakhulupirira. |
|
| 19 |
|
| A nyumba ya Israyeli inu, lemekezani Yehova: A nyumba ya Aroni inu, lemekezani Yehova: |
|
| 20 |
|
| A nyumba ya Levi inu, lemekezani Yehova: Inu akuopa Yehova, lemekezani Yehova. |
|
| 21 |
|
| Alemekezedwe Yehova kucokera m'Ziyoni, Amene akhala m'Yerusalemu. Haleluya, |
|
|
|
|