|
| 1 |
|
| Yamikani Yehova chifukwa ndi wabwino. Pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya. |
|
| 2 |
|
| Yamikani Mulungu wa milungu. Pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya. |
|
| 3 |
|
| Yamikani Ambuye wa ambuye, pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya. |
|
| 4 |
|
| Iye yekhayo amene amachita zodabwitsa zazikulu, pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya. |
|
| 5 |
|
| Amene mwachidziwitso chake anapanga mayiko akumwamba, pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya. |
|
| 6 |
|
| Amene anayala dziko lapansi pamwamba pa madzi, pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya. |
|
| 7 |
|
| Amene anapanga miyuni ikuluikulu, pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya. |
|
| 8 |
|
| Dzuwa lilamulire usana, pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya. |
|
| 9 |
|
| Mwezi ndi nyenyezi zilamulire usiku, pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya. |
|
| 10 |
|
| Amene anakantha ana woyamba kubadwa a Igupto, pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya. |
|
| 11 |
|
| Natulutsa Israeli pakati pawo, pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya. |
|
| 12 |
|
| Ndi dzanja lamphamvu ndi mkono wotambasuka, pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya. |
|
| 13 |
|
| Amene anagawa Nyanja Yofiira pakati, pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya. |
|
| 14 |
|
| Nadutsitsa Israeli pakati pa nyanjayo, pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya. |
|
| 15 |
|
| Koma anakokolola Farao ndi ankhondo ake mʼNyanja Yofiira, pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya. |
|
| 16 |
|
| Amene anatsogolera anthu ake mʼchipululu pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya. |
|
| 17 |
|
| Amene anakantha mafumu akuluakulu, pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya. |
|
| 18 |
|
| Napha mafumu amphamvu, pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya. |
|
| 19 |
|
| Siloni mfumu ya Aamori, pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya. |
|
| 20 |
|
| Ogi mfumu ya Basani, pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya. |
|
| 21 |
|
| Napereka dziko lawo ngati cholowa, pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya. |
|
| 22 |
|
| Cholowa cha mtumiki wake Israeli; pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya. |
|
| 23 |
|
| Amene anatikumbukira ife anthu opeputsidwa, pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya. |
|
| 24 |
|
| Amene anatimasula kwa adani athu, pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya. |
|
| 25 |
|
| Amene amapereka chakudya kwa cholengedwa chilichonse, pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya. |
|
| 26 |
|
| Yamikani Mulungu wakumwamba, pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya. |
|
|
|
|