|
| 1 |
|
| Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. Inu Yehova, mwandisanthula ndipo mukundidziwa. |
|
| 2 |
|
| Inu mumadziwa pamene ndikhala pansi ndi pamene ndidzuka; mumazindikira maganizo anga muli kutali. |
|
| 3 |
|
| Mumapenyetsetsa pamene ndikutuluka ndi kugona kwanga; mumadziwa njira zanga zonse. |
|
| 4 |
|
| Mawu asanatuluke pa lilime langa mumawadziwa bwinobwino, Inu Yehova. |
|
| 5 |
|
| Mumandizinga kumbuyo ndi kutsogolo komwe; mwasanjika dzanja lanu pa ine. |
|
| 6 |
|
| Nzeru zimenezi ndi zopitirira nzeru zanga, ndi zapamwamba kuti ine ndizipeze. |
|
| 7 |
|
| Kodi ndingapite kuti kufuna kuzemba Mzimu wanu? Kodi ndingathawire kuti kuchoka pamaso panu? |
|
| 8 |
|
| Ndikakwera kumwamba, Inu muli komweko; ndikakagona ku malo a anthu akufa, Inu muli komweko. |
|
| 9 |
|
| Ngati ndiwulukira kotulukira dzuwa, ngati ndikakhala ku malekezero a nyanja, |
|
| 10 |
|
| kumenekonso dzanja lanu lidzanditsogolera, dzanja lanu lamanja lidzandigwiriziza. |
|
| 11 |
|
| Ndikanena kuti, “Zoonadi, mdima udzandibisa ndithu ndipo kuwunika kukhale mdima mondizungulira,” |
|
| 12 |
|
| komabe mdimawo sudzakhala mdima kwa Inu; usiku udzawala ngati masana, pakuti mdima uli ngati kuwunika kwa Inu. |
|
| 13 |
|
| Pakuti Inu munalenga za mʼkati mwanga; munandiwumba pamodzi mʼmimba mwa amayi anga. |
|
| 14 |
|
| Ndimakuyamikani chifukwa ndinapangidwa mochititsa mantha ndi modabwitsa; ntchito zanu ndi zodabwitsa, zimenezi ndimazidziwa bwino lomwe. |
|
| 15 |
|
| Mapangidwe anga sanabisike pamaso panu pamene ndimapangidwa mʼmalo achinsinsi, pamene ndinkawumbidwa mwaluso mʼmimba ya amayi anga. |
|
| 16 |
|
| Maso anu anaona thupi langa lisanawumbidwe. Masiku onse amene anapatsidwa kwa ine, analembedwa mʼbuku lanu asanayambe nʼkuwerengedwa komwe. |
|
| 17 |
|
| Zolingalira zanu pa ine ndi zamtengowapatali, Inu Mulungu, ndi zosawerengeka ndithu! |
|
| 18 |
|
| Ndikanaziwerenga, zikanakhala zochuluka kuposa mchenga; pamene ndadzuka, ndili nanube. |
|
| 19 |
|
| Ndi bwino mukanangopha anthu oyipa, Inu Mulungu! Chokereni inu anthu owononga anzanu! |
|
| 20 |
|
| Amayankhula za Inu ndi zolinga zoyipa; adani anu amagwiritsa ntchito dzina lanu molakwika. |
|
| 21 |
|
| Kodi ine sindidana nawo amene amakudani, Inu Yehova? Kodi sindinyansidwa nawo amene amakuwukirani? |
|
| 22 |
|
| Ndimadana nawo kwathunthu; ndi adani anga. |
|
| 23 |
|
| Santhuleni, Inu Mulungu ndipo mudziwe mtima wanga; Yeseni ndipo mudziwe zolingalira zanga. |
|
| 24 |
|
| Onani ngati muli mayendedwe aliwonse oyipa mwa ine, ndipo munditsogolere mʼnjira yanu yamuyaya. |
|
|
|
|