Buku Lopatulika 1992
|
| 1 |
| Waucitsiru amati mumtima mwace, Kulibe Mulungu. Acita zobvunda, acita nchito zonyansa; Kulibe wakucita bwino. |
| 2 |
| Yehova m'Mwamba anaweramira pa ana a anthu, Kuti aone ngati aliko wanzeru, Wakufuna Mulungu. |
| 3 |
| Anapatuka onse; pamodzi anabvunda mtima; Palibe wakucita bwino ndi mmodzi yense. |
| 4 |
| Kodi onse ocita zopanda pace sadziwa kanthu? Pakudya anthu anga monga akudya mkate, Ndipo saitana pa Yehova. |
| 5 |
| Pamenepa anaopa-opatu: Pakuti Mulungu ali mu mbadwo wa wolungama. |
| 6 |
| Munyazitsa uphungu wa wozunzika, Koma Yehova ndiye pothawira pace. |
| 7 |
| Mwenzi cipulumutso ca Israyeli citacokera ku Ziyoni! Pakubweretsa Yehova anthu ace a m'nsinga, Pamenepo adzakondwera Yakobo, nadzasekera Israyeli. |
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa1992/psalms/014.mp3
150
14