×

Buku Loyera

MASALIMO 14

1
Mumtima mwake munthu wopusa amati, “Kulibe Mulungu.” Anthu otereŵa ndi oipa, amachita zonyansa, palibe ndi mmodzi yemwe wochita zabwino.
2
Chauta kumwambako waŵerama, akuyang'ana anthu pansi pano, kuti aone ngati angakhalepo mmodzi wanzeru wofunitsitsa Mulungu.
3
Koma ai, anthu onse ndi osokera, onsewo ndi oipa chimodzimodzi. Palibe ndi mmodzi yemwe wochita zabwino, ai, palibiretu ndi mmodzi yemwe.
4
Kani anthu oipaŵa alibe nzeru chotere? Iwo amameza anthu anga, kuŵayesa chakudya, ndipo samutama Chauta mopemba.
5
Tsonotu iwo adzachita mantha aakulu, pakuti Mulungu amakhala pa mbali ya anthu abwino.
6
Inu anthu oipa, mumayesa kusokoneza zolinga za anthu osauka, koma iwo amathaŵira kwa Chauta.
7
Chibwere ndithu chipulumutso cha Israele kuchokera ku Ziyoni. Chauta akadzaŵabwezera ufulu anthu ake, Yakobe adzakondwera, Israele adzasangalala kwambiri.
Chewa Bible BLYDC
Bible Society of Malawi
:
Sungani Zolemba