Buku Lopatulika 1992
|
| 1 |
| Ndilanditseni, Yehova, kwa munthu woipa; Ndisungeni kwa munthu waciwawa; |
| 2 |
| Amene adzipanga zoipa mumtima mwao; Masiku onse amemeza nkhondo. |
| 3 |
| Anola lilime lao ngati njoka; Pansi pa milomo yao pali ululu wa mphiri. |
| 4 |
| Ndilindireni Yehova, ndisalowe m'manja mwa woipa; Ndisungeni kwa munthu waciwawa; Kwa iwo akuti akankhe mapazi anga. |
| 5 |
| Odzikuzaanandichera msampha, nandibisira zingwe; Anacha ukonde m'mphepete mwa njira; Anandichera makwekwe. |
| 6 |
| Ndinati kwa Yehova, Inu ndinu Mulungu wanga; Mundicherere khutu mau a kupemba kwanga, Yehova. |
| 7 |
| Yehova Ambuye, ndinu mphamvu ya cipulumutso canga, Munandiphimba mutu wanga tsiku lakulimbana nkhondo. |
| 8 |
| Yehova, musampatse woipa zokhumba iye; Musamthandize zodzipanga zace; angadzikuze. |
| 9 |
| Kunena za mutu wao wa iwo akundizinga, Coipa ca milomo yao ciwaphimbe. |
| 10 |
| Makala amoto awagwere; Aponyedwe kumoto; M'maenje ozama, kuti asaukenso. |
| 11 |
| Munthu wamlomo sadzakhazikika pa dziko lapansi; Coipa cidzamsaka munthu waciwawa kuti cimgwetse. |
| 12 |
| Ndidziwa kuti Yehova adzanenera wozunzika mlandu, Ndi kuweruzira aumphawi, |
| 13 |
| Indedi, olungama adzayamika dzina lanu; Oongoka mtima adzakhala pamaso panu, |
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa1992/psalms/140.mp3
150
140