Buku Lopatulika 1992
|
| 1 |
| Yehova, ndaitana kwa Inu; ndifulumireni ine; Mundicherere khutu, pamene ndiitana kwa Inu. |
| 2 |
| Pempherolanga liikike ngaticofukiza pamaso panu; Kukweza manja anga kuikike ngati nsembe ya madzulo. |
| 3 |
| Muike mdindo pakamwa panga, Yehova; Sungani pakhomo pa milomo yanga. |
| 4 |
| Mtima wanga usalinge ku cinthu coipa, Kucita nchito zoipa Ndi anthu akucita zopanda pace; Ndipo ndisadye zankhuli zao. |
| 5 |
| Akandipanda munthu wolungama ndidzati ncifundo: Akandidzudzula, ndidzakuyesa mafuta a pamutu; Mutu wanga usakane: Pakuti pangakhale posautsidwa iwo ndidzawapempherera. |
| 6 |
| Oweruza ao anagwetseka pambali pa thanthwe; Nadzamva mau anga kuti ndiwo okondweretsa. |
| 7 |
| Mafupa athu amwazika pakamwa pa manda, Monga ngati akumba nanyimphula nthaka yapansi. |
| 8 |
| Pakuti maso anga apenya kwanu, Yehova Ambuye; Ndithawira kwa Inu; musataye moyowanga. |
| 9 |
| Mundisunge ndisagwe mumsampha anandicherawo, Ndisakodwe m'makwekwe a iwo ocita zopanda pace, |
| 10 |
| Oipa agwe pamodzi m'maukonde ao, Kufikira nditapitirira ine. |
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa1992/psalms/141.mp3
150
141