Mawu a Mulungu 2016
|
| 1 |
| Salimo la Davide. Inu Yehova ndikukuyitanani; bwerani msanga kwa ine. Imvani mawu anga pamene ndiyitana Inu. |
| 2 |
| Pemphero langa lifike kwa Inu ngati lubani; kukweza manja kwanga kukhale ngati nsembe yamadzulo. |
| 3 |
| Yehova ikani mlonda pakamwa panga; londerani khomo la pa milomo yanga. |
| 4 |
| Musalole kuti mtima wanga ukokedwere ku zoyipa; kuchita ntchito zonyansa pamodzi ndi anthu amene amachita zoyipa; musalole kuti ndidye nawo zokoma zawo. |
| 5 |
| Munthu wolungama andikanthe, chimenecho ndiye chifundo; andidzudzule ndiye mafuta pa mutu wanga. Mutu wanga sudzakana zimenezi. Komabe pemphero langa nthawi zonse ndi lotsutsana ndi ntchito za anthu ochita zoyipa. |
| 6 |
| Olamulira awo adzaponyedwa pansi kuchokera pa malo okwera kwambiri, ndipo anthu oyipa adzaphunzira kuti mawu anga anayankhulidwa bwino. |
| 7 |
| Iwo adzati, “Monga momwe nkhuni zimamwazikira akaziwaza, ndi momwenso mafupa athu amwazikira pa khomo la manda.” |
| 8 |
| Koma maso anga akupenyetsetsa Inu Ambuye Wamphamvuzonse; ndimathawira kwa Inu, musandipereke ku imfa. |
| 9 |
| Mundipulumutse ku misampha imene anditchera, ku makhwekhwe amene anthu oyipa andikonzera. |
| 10 |
| Anthu oyipa akodwe mʼmaukonde awo, mpaka ine nditadutsa mwamtendere. |
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2016/psalms/141.mp3
150
141