Mawu a Mulungu 2016
|
| 1 |
| Ndakatulo ya Davide, pamene iyeyo anali mʼphanga. Pemphero. Ndikulirira Yehova mofuwula; ndikukweza mawu anga kwa Yehova kupempha chifundo. |
| 2 |
| Ndikukhuthula madandawulo anga pamaso pake; ndikufotokoza za masautso anga pamaso pake. |
| 3 |
| Pamene mzimu wanga walefuka mʼkati mwanga, ndinu amene mudziwa njira yanga. Mʼnjira imene ndimayendamo anthu anditchera msampha mobisa. |
| 4 |
| Yangʼanani kumanja kwanga ndipo onani; palibe amene akukhudzika nane. Ndilibe pothawira; palibe amene amasamala za moyo wanga. |
| 5 |
| Ndilirira Inu Yehova; ndikuti, “Ndinu pothawirapo panga, gawo langa mʼdziko la anthu amoyo.” |
| 6 |
| Mverani kulira kwanga pakuti ndathedwa nzeru; pulumutseni kwa amene akundithamangitsa pakuti ndi amphamvu kuposa ine. |
| 7 |
| Tulutseni mʼndende yanga kuti nditamande dzina lanu. Ndipo anthu olungama adzandizungulira chifukwa cha zabwino zanu pa ine. |
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2016/psalms/142.mp3
150
142