Buku Loyera
|
| 1 |
| Ndikulirira Chauta mokweza, ndikupemba kwa Chauta mofuula. |
| 2 |
| Ndikupereka madandaulo anga kwa Iye, ndikutchula mavuto anga pamaso pake. |
| 3 |
| Pamene mtima wanga ufooka, Inu mumadziŵa zoti ndichite. Adani anditchera msampha m'njira imene ndimayendamo. |
| 4 |
| Ndikayang'ana ku dzanja lamanja, palibe ndi mmodzi yemwe wosamalako za ine. Kulibe koti ndithaŵire, palibe munthu wondisamala. |
| 5 |
| Ndimalirira Inu Chauta, ndimati, “Inu ndinu kothaŵira kwanga, ndinu zanga zonse m'dziko la amoyo.” |
| 6 |
| Imvani kulira kwanga, pakuti ndataya mtima. Pulumutseni kwa ondizunza, chifukwa andiposa mphamvu. |
| 7 |
| Tulutseni m'ndende kuti ndizitamanda dzina lanu. Anthu anu adzandizungulira, chifukwa Inu mwandichitira zabwino zambiri. |
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewablydc/psalms/142.mp3
150
142