Buku Loyera
|
| 1 |
| Atamandike Chauta, thanthwe langa londitchinjiriza, amene amaphunzitsa manja anga ndi zala zanga kumenya nkhondo. |
| 2 |
| Ndiye thanthwe langa ndi tchemba langa londiteteza, ndiye linga langa londipulumutsa, ndiye chishango changa chothaŵirako. Amaika mitundu ya anthu mu ulamuliro wanga. |
| 3 |
| Inu Chauta, kodi munthu nchiyani, kuti muzimsamala? Mwana wa munthu nchiyani, kuti muzimganizira? |
| 4 |
| Munthu ali ngati mpweya, masiku ake ali ngati mthunzi wosakhalitsa. |
| 5 |
| Ng'ambani thambo, Inu Chauta, ndi kutsikira pansi. Khudzani mapiri kuti afuke nthunzi. |
| 6 |
| Ng'animitsani zing'aning'ani ndi kuŵamwaza adani anga. Ponyani mivi yanu, ndi kuŵapirikitsa. |
| 7 |
| Tambasulani dzanja lanu kuchokera kumwamba. Landitseni ndi kundipulumutsa ku madzi ozama, omboleni m'manja mwa akunja, |
| 8 |
| amene amalankhula zabodza, ndipo amalumbira zonama. |
| 9 |
| Ndidzakuimbirani nyimbo yatsopano, Inu Mulungu. Ndidzakuimbirani zeze wa nsambo khumi, |
| 10 |
| Inu amene mumapambanitsa mafumu pankhondo, amene mumalanditsa Davide mtumiki wanu. |
| 11 |
| Landitseni kwa adani ankhalwe, mundipulumutse m'manja mwa akunja, amene amalankhula zabodza, ndipo amalumbira zonama. |
| 12 |
| Ana athu aamuna pachinyamata pao akhale amphamvu ngati mitengo, ana athu aakazi akhale okongola ngati nsanamira zozokotedwa zapangodya, zoti zikometse nyumba yaufumu. |
| 13 |
| Nkhokwe zathu zikhale zodzaza, zisunge zokolola za mtundu uliwonse. Nkhosa zathu zibale ana zikwizikwi m'mabusa athu. |
| 14 |
| Ng'ombe zathu zikhale ndi maŵele, zisapoloze kapena kulephera kubereka. M'miseu mwathu musakhale kulira chifukwa cha mavuto. |
| 15 |
| Ngodala anthu olandira madalitso ameneŵa. Ngodala anthu amene Mulungu wao ndi Chauta. |
|
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewablydc/psalms/144.mp3
150
144