Buku Loyera
|
| 1 |
| Tamandani Chauta! Nkwabwino kuimba nyimbo zotamanda Mulungu wathu, nkokondwetsa mtima kumtamanda moyenera. |
| 2 |
| Chauta akumanga Yerusalemu, akusonkhanitsa Aisraele omwazika. |
| 3 |
| Akuchiritsa a mtima wachisoni, ndipo akumanga mabala ao. |
| 4 |
| Amadziŵa chiŵerengero cha nyenyezi, zonse amazitcha maina ake. |
| 5 |
| Mbuye wathu ndi wamkulu, ndipo ndi wa mphamvu zambiri, nzeru zake nzopanda malire. |
| 6 |
| Amakweza oponderezedwa, koma amagwetsa pansi anthu oipa. |
| 7 |
| Imbirani Chauta mothokoza, imbirani Mulungu wathu nyimbo yokoma ndi pangwe. |
| 8 |
| Amaphimba zakumwamba ndi mitambo, amapatsa nthaka mvula, amameretsa udzu pa magomo. |
| 9 |
| Amapereka chakudya kwa nyama ndi kwa ana a khungubwi pamene akulira chakudya. |
| 10 |
| Mphamvu za kavalo saziyesa kanthu, mphamvu za ankhondo sazisamala. |
| 11 |
| Koma Chauta amakondwera ndi anthu omuwopa, amene amadalira chikondi chake chosasinthika. |
| 12 |
| Tamanda Chauta, iwe Yerusalemu. Tamanda Mulungu wako, iwe Ziyoni. |
| 13 |
| Paja amalimbitsa mipiringidzo ya zipata zako. Amadalitsa anthu amene ali mwa iwe. |
| 14 |
| Amadzetsa mtendere m'malire a dziko lako, amakudyetsa pokupatsa ufa wa tirigu wosalala. |
| 15 |
| Akapereka lamulo pa dziko lapansi, mau ake amayenda mwaliŵiro. |
| 16 |
| Amagwetsa chisanu chambee ngati ubweya. Amamwaza chipale ngati phulusa. |
| 17 |
| Amagwetsa matalala ngati miyala. Kodi ndani angathe kupirira kuzizira kwake? |
| 18 |
| Akalamula kuti zichoke, pomwepo zimasungunuka, akaombetsa mphepo, madzi amayenda. |
| 19 |
| Amadziŵitsa Yakobe mau ake, amaphunzitsa Israele malamulo ake ndi malangizo ake. |
| 20 |
| Sadachitepo zimenezi ndi mtundu wina uliwonse wa anthu, iwo sadziŵa malangizo ake. Tamandani Chauta! |
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewablydc/psalms/147.mp3
150
147