Buku Lopatulika 1992
|
| 1 |
| Haleluya. Lemekezani Yehova kocokera kumwamba; Mlemekezeni m'misanje. |
| 2 |
| Mlemekezeni, angelo ace onse; Mlemekezeni, makamu ace onse. |
| 3 |
| Mlemekezeni, dzuwa ndi mwezi; Mlemekezeni, nyenyezi zonse zaunikira. |
| 4 |
| Mlemekezeni, m'mwambamwamba, Ndi madzi inu, a pamwamba pa thambo. |
| 5 |
| Alemekeze dzina la Yehova; Popeza analamulira, ndipo zinalengedwa. |
| 6 |
| Anazikhazikanso ku nthawi za nthawi; Anazipatsa cilamulo cosatumphika. |
| 7 |
| Lemekezani Yehova kocokera ku dziko lapansi, Zinsomba inu, ndi malo ozama onse; |
| 8 |
| Moto ndi matalala, cipale cofewa ndi nkhungu; Mphepo ya namondwe, yakucita mau ace; |
| 9 |
| Mapiri ndi zitunda zonse; Mitengo yazipatso ndi yamikungudza yonse: |
| 10 |
| Nyama za kuthengo ndi zoweta zonse; Zokwawa, ndi mbalame zakuuluka; |
| 11 |
| Mafumu a padziko ndi mitundu yonse ya anthu; Zinduna ndi oweruza onse a padziko; |
| 12 |
| Anyamata ndiponso anamwali; Okalamba pamodzi ndi ana: |
| 13 |
| Alemekeze dzina la Yehova; Pakuti dzina lace lokha ndi lokwezeka; Ulemerero wace uli pamwamba pa dziko lapansi ndi thambo. |
| 14 |
| Ndipo anakweza nyanga ya anthu ace, Cilemekezo ca okondedwa ace onse; Ndiwo ana a Israyeli, anthu a pafupi pa Iye, Haleluya, |
|
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa1992/psalms/148.mp3
150
148