Buku Loyera
|
| 1 |
| Inu Chauta, kodi ndani angathe kukhala m'Nyumba mwanu? Ndani angathe kukhala pa phiri lanu loyera? |
| 2 |
| Ndi munthu amene amayenda mosalakwa, amene amachita zolungama nthaŵi zonse, amene amalankhula zinthu ndi mtima woona. |
| 3 |
| Ndi amene sasinjirira ndipo sachita anzake zoipa, kapena kumafalitsa mbiri yoipa ya anzake. |
| 4 |
| Ndi amene amanyoza munthu womkana Mulungu, koma amalemekeza anthu omvera Chauta. Ndi amene amachitadi zimene walonjeza, ngakhale zikhale zoŵaŵa chotani. |
| 5 |
| Ndi amene sakongoza ndalama zake kuti alandire chiwongoladzanja, amene salandira chiphuphu kuti azunze munthu wosalakwa. Munthu wochita zimenezi, palibe chilichonse chimene chidzamgwedeze. |
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewablydc/psalms/015.mp3
150
15